"SULOM YANGOMUDA DE JONGH" - SILVER
Timu ya Silver Strikers yalemba kalata ya masamba asanu ndi imodzi (6) ku bungwe la Super league of Malawi kuti lichotse milandu yomwe yaikidwa kwa mphunzitsi wawo, Peter De Jongh kamba koti zaonetsa kumuda, kumuipitsira mbiri, kumusala, kusayendetsa bwino komanso kukondera kwa anthu ena.
Mukalatayi, timuyi yati SULOM sinafunse okhudzidwa pa nkhaniyi monga omwe amayang'anira masewerowa, oyimbira, apolisi, achitetezo ndi ena komanso sanapereke kalata iliyonse kutimuyi maola 72 asanakayankhe milanduyi monga mwa lamulo.
Iyo yati De Jongh anangothamanga mu bwalo la zamasewero pomwe ena sanafunsidwepo ngati matimu a Wanderers ndi Tigers anamenyanako, Bullets inalowa cha futa mmbuyo ndi bus komanso mmabwalo ena.
Timuyi yati mmene bungwe la SULOM likugwirira ntchito, ndi zosiyana ndi mfundo zomwe mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya, ananena kuti asintha kumpira waku Malawi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores