OSEWERA A FLAMES AKUCHITA BWINO KU COSAFA
Timu ya Malawi yasonkha asanu pa osewera khumi ndi mmodzi omwe bungwe la Confederations of Southern Africa Football Associations (COSAFA) lasankha kuti asewera bwino mu ndime ya mmagulu ku mpikisanowu.
Timu ya Flames ndi yokhayo yomwe yapambana masewero onse atatu komanso osagoletsetsa chigoli chilichonse ndipo osewera awo anachita bwino mmasewero awo.
Goloboyi, Brighton Munthali, otseka kumbuyo Dennis Chembezi ndi Alick Lungu komanso omwetsa zigoli Lanjesi Nkhoma ndi Chawanangwa Kaonga ndi omwe asankhidwa mutimuyi.
Kuchita bwino kwa timuyi kwapangitsa kufika mu ndime yamatimu anayi kumpikisanowu pomwe akumane ndi timu ya dziko la Lesotho lachisanu likudzali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores