NYAMILANDU ATHA KUPEZA MPANDO KU CAF
Mtsogoleri wa timu ya Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, akhonza kupeza mpando mu komiti yaikulu ku bungwe la Confederations of African Football pomwe akupikisana ndi anzake awiri pa chisankho cha lero.
Nyamilandu akupikisana ndi mtsogoleri wa bungwe loyendetsa masewero ku Lesotho, Mokhosi Philip Mahapi komanso waku Mauritius, Mohammed Ally Samir Sobha pa woyimilira mabungwe akummwera kwa Africa kuno.
Zisankhozi zichitika lero pomwe kuli mkumano waukulu ku bungwe la CAF ndipo akhalenso akusankha atsogoleri a mmakomiti osiyanasiyana ku Abidjan mdziko la Cote d'Ivoire.
Iye anakhalaponso mmodzi wamu khonsolo la FIFA mu zaka za mmbuyomu ndipo akhonza kupezanso mpando waku FAM kachisanu mmwezi wa December mu chisankho cha FAM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores