"MABEDI NDI KATUNDU" - NYAMILANDU
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Walter MacMillan Nyamilandu Manda, wayamikira mphunzitsi wogwirizira watimu ya Flames, Patrick Mabedi poitsogolera kuti timuyi ichite bwino ku mpikisano wa COSAFA wa chaka chino.
Nyamilandu amayankhula izi pomwe timuyi yangotsala ndi masewero awiri okha kuti apambane chikhochi koyamba mu mbiri ya mpira ndipo yagonjetsa matimu onse omwe akumana nawo.
Iye wati Mabedi wabweretsa kusintha kwakukulu kutimuyi ndipo wayamikira aphunzitsi ndi osewera polimbikira.
"Aphunzitsi onse otsogozedwa ndi Mabedi komanso osewera achita bwino kwambiri ndipo abweretsa Chimwemwe kwa ife. Chifukwa choti tinasintha aphunzitsi, kaseweredwe Kasintha ndipo abweretsa katsopano komwe osewera akukatha." Anatero Walter.
Mabedi analowa mmalo mwa Mario Marian Marinica yemwe waphunzitsa timuyi kuchokera mu 2022 koma zipatso sizimaoneka. Iye wapambanako masewero atatu ndi kufanana mphamvu kawiri pa masewero asanu ake kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores