ZIKHULUPILIRO MU MPIRA ZAVUTA KU MALAWI
Zikhulupiliro zafikapo mu masewero a mpira wamiyendo ku Malawi pomwe sabata yathayi zinaliponso mu ligi ya TNM makamaka pa bwalo la Karonga.
Loweruka, timu ya Kamuzu Barracks, inathira mkodzo pa golo la timu ya Chitipa United ati poganizira kuti eni khomowa anali ndi mankhwala omwe amakanikitsa timuyi kugoletsa.
Ndipo lamulungu, mmodzi mwa akuluakulu a timu ya Dedza Dynamos anapezeka ndi chinthu chomwe akuganizira kuti ndi chithumwa pomwe timuyi inagonja 2-1 ndi Karonga United.
Mu ligi ya chaka chino, zikhulupiliro zikuchitika kwambiri koma palibe timu Ina iliyonse yomwe yalandirako zilango za mchitidwewu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores