NYONDO WATSOGOLA NDI ZIGOLI
Katswiri wa timu ya Dedza Dynamos, Clement Nyondo, tsopano akutsogola pa ndandanda wa osewera omwe agoletsa zigoli zambiri mu ligi ya TNM pomwe ali ndi zigoli zisanu ndi zinayi (9) mu ligiyi.
Nyondo anagoletsa chigoli choonjezera pa masewero omwe timu yake inagonja 2-1 ndi timu yake yakale ya Karonga United pa bwalo la Karonga lamulungu.
Iye tsopano akutsogola pomwe Lanjesi Nkhoma ali ndi zigoli 8 pambuyo Pake komanso Christopher Kumwembe ndi Stain Davie ali ndi zisanu ndi ziwiri (7) aliyense.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores