"DE JONGH AKAPHUNZIRE MPIRA WAKU MALAWI" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald 'Nginde' Mtetemera, wati akupita ku Lilongwe ndi cholinga chimodzi chokatenga ma points atatu basi pomwe akukumana ndi Silver Strikers mu ligi ya TNM loweruka pa bwalo la Bingu.
Mtetemera wati alibe mantha aliwonse kukumana ndi ma Banker ndipo akonzekere kusenza thumba la misomali pomwe iye akamuphunzitse waku mpanje.
"Timu ilibwino ndipo chilichonse chili mchimake, ulendo tanyamuka kuti tikapeze chipambano tizibwerako. Uyu [De Jongh] samaudziwa mpira waku Malawi ndipo loweruka lino akawudziwa mmene umaseweredwera." Anatero Nginde.
Timu ya Chitipa United inapereka mabala owawa kumatimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets pomwe anawathira kugonja kwawo koyamba chaka chino mu ligi. Timu ya Silver ndi yokhayo imene sinalaweko kugonja ndipo ikupita masewerowa ikutsogola ndi 24 points pa nambala yoyamba kusiyana ma points asanu ndi atatu (8) ndi Chitipa United.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores