"MASAPOTA A KU CHITIPA NDI OZINDIKIRA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald'Nginde'Mtetemera wati masapota atimu yake ndi ozindikira kusiyana ndi masapota a matimu ena pomwe wati amamvetsetsa zotsatira za masewero.
Mtetemera amayankhula izi atatha masewero awo pomwe anagonja 1-0 ndi Dedza Dynamos pa bwalo la Karonga kuti atuluke mu chikho cha FDH Bank lachitatu. Iye anati ochemerera atimuyi samawafinya kwambiri kuti azichita bwino poti timu yawo ikadali ya ana.
"Kwa masapota aku Chitipa ndi ozindikira kusiyana ndi amatimu enawa ndipo amadziwa kuti kumpira kuli kupambana, kufanana mphamvu ndi kugonja nde lero tagonja, tachivomereza. Ndimanena mobwereza kuti timu yathu ndi yachisodzera nde tikadaphunzirabe, mwina zimangochitika tikapambana kuti mwina tsiku limenelo kwacha bwino nde sindimayembekezera zambiri kwa anyamatawa." Anatero Nginde.
Mtetemera anayankhula izi pomwe masapota a Mighty Mukuru Wanderers akumachitira za ntopola osewera awo akagonja kapena kufa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores