CHAWANANGWA WAPATSIDWA NAMBALA 10 KU ZANACO
Katswiri watimu ya Flames, Chawanangwa Kaonga, wapatsidwa nambala 10 yapa malaya ake omwe azivala ku timu ya ZANACO ku Zambia mu ligi ya chaka chino.
Kaonga wapatsidwa nambalayi kutsatira kuchita bwino kumpikisano wa COSAFA Cup wa chaka chino pomwe anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mu mpikisanowu.
Iye anavala malayawa koyamba loweruka pomwe timuyi imasewera ndi Red Arrows ndipo anagoletsa chigoli cha timuyi pomwe inagonja 3-1 mu mpikisano wa matimu anayi.
Iye anavalanso kachiwiri pomwe dzulo anasewera masewero omwe timu yake inafanana mphamvu ndi Zesco United 0-0.
Ligi ya mdziko la Zambia ikhale ikuyamba mu mwezi omwe uno ndipo timu ya ZANACO iziyang'ana kwambiri pa Kaonga.
Good
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores