WANDERERS YACHOTSA STEVE PALAMEZA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yalengeza kuti yasiyana ndi mmodzi mwa akuluakulu kutimuyi, Steve Palameza, atamupeza olakwa pa milandu Ina yosowa khalidwe kutimuyi.
Mu kalata yomwe timuyi yapereka kwa Palameza, yamuuza kuti amuchotsa kamba ka milandu itatu yomwe anavomera kuti ndi olakwa pa 19 September 2023, akuluakulu ena oona zakhalidwe atamuitana.
Mmalipoti ena, zamveka kuti iye ndi amene anasowetsa K60 million ku timuyi pomwe amakatenga ngongole mu dzina la timuyi.
Source: Times
Ndidzoona รกsowe