BULLETS YAPEZA WOTHANDIZA MPHOTO ZAPAMWEZI
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti yalowa mu mgwirizano wa chaka chimodzi ndi kampani ya BCA Travel and Tours yomwe izithandiza mphoto za osewera wapamwamba kutimuyi.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi lachisanu pomwe zonse za mgwirizanowu zatheka.
Mkulu wa anthu ogwira ntchito kutimuyi Albert Chigoga wati zimakhala zinthu zopambana kuyamikira ntchito za osewera zomwe akukhulupilira kuti zipereka chilimbikitso chachikulu kutimuyi.
"Ndili ndi chikhulupiliro kuti mphoto zimenezi zithandizire kupititsa patsogolo momwe timu izichitira mu masewero ake," anatero Chigoga.
Kampaniyi izipereka ka chikho komanso ndalama yokwana K1 million Kwa osewera yemwe azipambana mphotoyi makamaka kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores