Timu ya Namitete Zitha yatsimikiza kuti mphunzitsi wawo, Kenwood Nkhoma, wachoka kutimuyi pomwe wapita kutimu ya Kamuzu Barracks.
Nkhoma watsogolera timuyi masewero amodzi okha chabe omwe timuyi yagonja ndi Extreme FC 1-0 mu masewero otsegulira ligi mu NBS Bank National Division League.
Timuyi yamufunira zabwino mphunzitsiyu pomwe akupita mu FDH Premiership kuti akalowe mmalo mwa Tione Mhone yemwe wayimitsidwa pa ntchito yake.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores