Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"ANYAMATA ANALI ACHILENDO NDI BWALO" - KAMANGENI
Mphunzitsi watimu ya Mulomba FC yaku Chikwawa, wati anyamata ake asewera bwino kwambiri koma amaliona bwalo la Mpira kukhala lachilendo mmasewero awo omwe agonja 1-2 ndi Durban FC lachinayi masana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe achititsa kuti asiyane ndi chikho cha Castel Challenge koma kupatula za bwalo, iye wati ndondomeko yosainira mapepala a osewera awo sinayende bwino yomwe yachititsa kuti osewera ena asasewere nawo mmasewerowa.
"Anzathu a FAM anabweretsa ma kadi mochedwa zomwe zapangitsa kuti osewera ena athu makadi awo asowe olo pepala lokatenga pa boma pathu takatenga lero komanso zama ID zapanga lero lomwe lino nde kukonzekera kwathu kunali kovutirapo moti osewera athu ena ali kumtunda uko nde zakhala ngati zatisokoneza." Anatero.
Timuyi inali akatswiri a boma la Chikwawa kutsatira kuchita bwino mmasewero awo mu bomali ndipo zateremu tsopano yatuluka mu mpikisanowu ndipo Kamangeni wati waphunziramo zambiri mu mpikisan