Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
FLAMES DROP ON FIFA RANKINGS
Malawi National Football team has dropped with three steps in the latest Coca-Cola World FIFA rankings released today.
The team was on position 122 but has dropped to 125 in April following poor outing in the Four Nations tournament last month.
The team lost 4-0 to Kenya which has gone four steps up to 107 and then were beaten 2-1 by Zambia. Zimbabwe has gone two steps up to position 122 after beating Zambia in the same tournament.
Uganda remain on position 92 while Zambia moves a step up to 86th in the rankings after beating Malawi in the tournament.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
MUNTHALI NDI CHAWANANGWA SAPEZEKA KWA MASABATA ATATU
Osewera awiri atimu ya Flames omwe amasewera kunja kwa dziko lino, Chawanangwa Kaonga ndi Brighton Munthali akhala masabata atatu asakugunda mpira kamba koti anavulala mmasewero omwe timuyi yalepherana 2-2 ndi Guinea loweruka pa bwalo la Bingu.
Munthali anavulala mchigawo choyamba ndipo anasinthana ndi Clever Nkungula pomwe Chawanangwa anavulala mu nthawi yoonjezera atagundana ndi osewera a Guinea.
Osewera onsewa athandizidwa ndipo auzidwa kuti asasewere kwa masabata atatu ndipo akaunikidwanso akapita ku matimu awo. Chawanangwa amasewera timu ya ZANACO ku Zambia pomwe Munthali ndi goloboyi wa Black Leopards yaku South Africa.
#Tawonga2023
SAIZI NDI CHAZIYA AMWETSA ZIGOLI ZOYAMBA KU FLAMES
Osewera atimu ya Flames, Robert Saizi komanso Lawrence Chaziya, atsegula matumba awo azigoli kutimuyi pomwe anamwetsa chigoli chimodzi aliyense kuti Flames ilepherane 2-2 ndi Guinea pa bwalo la Bingu loweruka masana.
Saizi anamwetsa chigoli chake choyamba ndi timuyi pa mphindi 23 anamalizitsa mpira omwe Lanjesi Nkhoma anamenyetsa munthu mu masewero ake achisanu ndi timuyi. Malawi inagoletsetsa zigoli ziwiri mu mphindi zitatu pomwe Aguibou Camara komanso Saidou Sow anamwetsa zigoli pa mphindi 56 ndi 58 aliyense kuti Guinea itsogole 2-1.
Masewero akupita kumapeto, Saizi anamenya Kona yomwe Chaziya anasumbira mu ukonde kuti apezenso Chigoli chake choyamba ndi timuyi mmasewero ake achikhumi chomwe chaletsa Flames kugonja.
Mu gulu la timuyi, Flames yathera pachitatu ndi mapointsi asanu pa masewero asanu ndi amodzi ndipo Egypt ndi Guinea ndi omwe achoka mu gululi ndikupita ku mpikisano wa African Cup of Nations wa 2023.
malawi tiyeni tilimbikikle
BANDA WAYAMIKIRA OSEWERA ACHISODZERA KU FLAMES
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya Flames, John Banda, wayamikira osewera omwe ndi achisodzera kutimuyi kamba kochita bwino ndi timuyi ku mpikisano wa COSAFA komwe anathera pa nambala yachinayi.
Banda amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Guinea yomwe iye walonjeza kuti iwo apanga kuthekera kulikonse kuti apambane.
Iye wati osewera achisodzera akuchita bwino kwambiri kutimuyi ndipo ngati angagwirane manja ndi achiyambakale akutimuyi, timuyi ipambana masewerowa.
Malawi ikukumana ndi Guinea mu masewero opitira ku mpikisano wa African Cup of Nations koma matimu omwe anadutsa kale ndi Egypt komanso Guinea yomweyi.
MABEDI AKUFUNIDWA KU SOUTH AFRICA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Flames, Patrick Mabedi, wati chitsogolo chake ndi chosadziwika bwinobwino pomwe matimu ena amdziko la South Africa akumufuna kuti akaphunzitse kumeneko.
Mgwirizano wa mphunzitsiyu utha mmwezi wa September ndipo iye wati zili ndi bungwe la Football Association of Malawi kuonjezera mgwirizano wake.
"Zonse zili mmanja mwa FAM komano chitsogolo sichikudziwikabe chifukwa matimu ena amu PSL akundifunanso nde tidikirabe ku likuluko." Anatero Mabedi.
Mphunzitsiyu yemwe waphunzitsapo matimu ena ngati Kaizer Chiefs komanso Moloka Swallows ku South Africa, anatenga timu ya Flames mu mwezi wa June kutsatira kutha kwa mgwirizano wa Mario Marinica.
Iye watsogolera Flames mmasewero asanu ndi awiri (7) ndipo sanagonjepo pa mphindi 90 za mkati mwa masewero.
MABEDI HAPPY WITH FLAMES' UNBEATEN IN 90 MINUTES
Malawi National Football team caretaker coach, Patrick Mabedi, has praised his boys for a brilliant performance at the COSAFA Cup in South Africa despite finishing fourth in the tournament.
The team lost 5-3 on penalties in the third place match after Christopher Kumwembe missed his penalty against South Africa. Meanwhile, the team has never lost a match in 90 minutes as their defeats in the Semi finals and third place have come through penalties to the delightfulness of Mabedi.
"If it was a league we could have been crowned Champions because we haven't lost a match. I am very proud of my boys we will come back stronger." Mabedi said.
The team finished as group winners in their group after amassing 9 points from three wins but lost to Lesotho 3-0 on penalties after a 1-1 draw in the 90 minutes and also lost to South Africa on Sunday through penalties as well.
Thanks Patrick u did it well n congratulations for that ,the team is gud now just teach them how to shoot 🔫 penalties
MARINICA WAYAMIKIRA MABEDI
Mphunzitsi wakale watimu yampira wamiyendo ya dziko lino Marian Mario Marinica wayamikira Patrick Mabedi kamba kochita bwino ndi timu ya Flames kumpikisano wa Cosafa wachaka chino omwe ukuchitikira ku Durban dziko la South Africa.
Malawi yalephera kufika ndime yotsiriza ya mpikisanowu dzulo pomwe yafa 3-0 kudzera pa mapenalty mumphindi 90 masewero anathera 1-1 koma inapambana masewero onse a mugulu kuti ifike mu ndimeyi.
Marinica wati Mabedi ndi mphunzitsi wabwino kwambiri ndi chifukwa chake iye anamutenga kuti akhale omuthandizira pa nthawi yake kutimuyi.
"Ndiyamikire Mabedi komanso anyamata pantchito yotamandika yomwe agwira kumpikisano wachaka chino, Palibe yemwe amapereka mpata kuti angachite motere. Mabedi ndimphunzitsi odziwa pantchito yache ndiye chifukwa munthawi yomwe ndinali mphunzitsi wa Malawi ndinamukhulupilira kuti akhale wachiwiri wanga," watero Marinica kuuza Garry Chirwa wa Nation Newspaper.
Malawi ikumana ndi South Africa loweruka
NYASULU IN A DAY TO REMEMBER
Flames goalkeeper, Innocent Nyasulu, had a mixed a day on Friday after making his first appearance in Red colours as he was trusted to make saves in the penalty shootout but saved none as the Flames lost 3-0 to Lesotho.
Nyasulu was introduced on 86th minute for first choice, Brighton Munthali as the game was tied on 1-1 when the coach was planning for penalty shootouts.
Nyasulu went to wrong directions in two kicks but could not save the final one from the opponent's goalkeeper, who saved three penalties for his team.
This was the first minutes for Nyasulu who has been trusted to be Flames' second Choice by Patrick Mabedi but his introduction has been criticized by People in Malawi.
MABEDI CONGRATULATES PLAYERS DESPITE LOSS
Malawi National team head coach, Patrick Mabedi had congratulated his charges after a brilliant showing at the COSAFA Cup despite the team's failure to reach into the final.
Flames lost 3-0 on penalties to Lesotho after a 1-1 draw in the 90 minutes despite having a numerical advantage as Lesotho played with a man less due to a red card.
After the game, Mabedi said his players failed to use their chances in the match but their display was very good.
"I have to give credit to my players. They did their best and we struggled to penetrate Lesotho defence as they dug deep. We had opportunities too but we missed them. We were not composed enough. Sometimes you need to be patient and not be rushing. But all in all we did all we could. It just wasn't our day." Said Mabedi.
The team will play South Africa on Saturday in the tournament's third place match.
MBC IWONETSA MASEWERO A MALAWI
Kanema wa dziko la Malawi, Malawi Broadcasting Corporation (MBC) walengeza kuti awonetsa masewero apakati pa Malawi ndi Lesotho omwe ndi ndime yamatimu anayi kumpikisano wa COSAFA mdziko la South Africa.
Mmodzi mwa akuluakulu a kanemayi, Chisomo Mwamadi, wati iwo apeza chilolezo choulutsa masewerowa pa MBC Tv, MBC 2 On the Go komanso Radio 2. Iye watinso ngati timuyi ifike ndime yotsiriza, iwo adzaonetsanso.
"Timu ya Flames yachita bwino kwambiri kumpikisanoeu, nde tinayesetsa ngati MBC kuti Mmalawi aliyense chimwemwechi chisamuphonye ndipo ndife okondwa kuti awonera pa MBC. Ngati Malawi ifike mu ndime yotsiriza ndekuti lamulungu adzawoneranso." Anatero Mwamadi.
Iye wati uwu ndi mwayi kuti makampani akatsatse malonda awo. Malawi ndi Lesotho onse anatsogolera gulu B ndi C aliyense kuti afike mu ndimeyi.
OSEWERA A FLAMES AKUCHITA BWINO KU COSAFA
Timu ya Malawi yasonkha asanu pa osewera khumi ndi mmodzi omwe bungwe la Confederations of Southern Africa Football Associations (COSAFA) lasankha kuti asewera bwino mu ndime ya mmagulu ku mpikisanowu.
Timu ya Flames ndi yokhayo yomwe yapambana masewero onse atatu komanso osagoletsetsa chigoli chilichonse ndipo osewera awo anachita bwino mmasewero awo.
Goloboyi, Brighton Munthali, otseka kumbuyo Dennis Chembezi ndi Alick Lungu komanso omwetsa zigoli Lanjesi Nkhoma ndi Chawanangwa Kaonga ndi omwe asankhidwa mutimuyi.
Kuchita bwino kwa timuyi kwapangitsa kufika mu ndime yamatimu anayi kumpikisanowu pomwe akumane ndi timu ya dziko la Lesotho lachisanu likudzali.
MALAWI COULD START DREAMING FOR THE WORLD CUP
Malawi National Football team, Flames, have been placed in what it looks like a fair group in the 2026 World Cup Qualifiers in a draw that has been conducted by Confederations of African Football on Thursday evening.
Malawi has been paired with Tunisia as top seeded team in Group H while Equatorial Guinea, Namibia, Liberia and Sao Tome and Principe are other teams in the group.
One of the Sports analysts in the country, Justin Mitambo, says this is just fair for Malawi and they can surely qualify for the World tournament.
"Surely, the draw had favoured us, we only have Tunisia as a tough opponent but with the confident the team has now after performing well at the COSAFA Cup, we can stop them. The other teams are average ones while the likes of São Tome are our samousa." Said Mitambo.
In the latest changes of the qualifications, the winners of each groups will go straight to the World Cup. Malawi has never been at the tournament.
Maravihossa 🙄🇲🇼
"CHIZUNGU CHIKUFUNIKIRA PA ANTHU" - LIWEWE
Mmodzi mwa atolankhani a nkhani zamasewero mdziko muno, Steve Liwewe Banda, wati makono anthu akufunikira kudziwako kachingerezi pang'ono ndi cholinga choti azilumikizana ndi anthu ammayiko osiyanasiyana poti chiyankhulochi chimagwiritsidwa ntchito mmayiko ambiri.
Liwewe amayankhula izi kutsatira katswiri wa timu ya Flames, Alick Lungu, anakanika kuyankhula mu chingerezi pomwe anasewera bwino mmasewero atimuyi ndi Zambia ku COSAFA ndipo James Sangala ndiye amamutanthauzira.
Liwewe wati ndi zofunika kuti anthu adziweko ngakhale pang'ono chingerezi poti zinthu zambiri monga kufunsira ntchito, kukambirana mu nyumba ya malamulo komanso ndondomeko za mankhwala ndi zina zimakhala mchingerezi.
"Kumangofunika kudziwako chingerezi pang'ono ngakhale utaphotchola amvabe kuti ukufuna chiyani. Chosangalatsa pano nchakuti ife makolo ngakhale sukulu inativuta timayesetsa kuti ana athu aphunzire chizungu." Anatero Liwewe.
Zabwino zonse timakunyadilani ngakhale mutaluza tilinanu
Mphunzitsi wamkulu ongogwilizira wa team ya dziko lino ya Flames, Patrick Mabedi wasankha mphunzitsi wa Blue Eagles, Elia Kananji kukhala wachiwiri wake ku team ya Flames.
Mabedi wasankhaso wachiwiri kwa mphunzitsi wa Silver Strikers, Peter Mgangira kukhala omuthangatira wachiwiri.
Malipoti akusonyezaso kuti Steve Madeira wasankhidwaso ngati team manager.
Flames drop 3 places on FIFA Ranking
Malawi National Football Team has dropped three places on the latest FIFA Ranking released today.
The Flames are now on position 127 from 124.
Morocco (#11) are the highest ranked team in Africa whereas Argentina are top ranked team in the World.
Bungwe la FAM latsimikiza kuti silionjezera mgwirizano wake ndi mphunzitsi wa timu ya Flames Mario Marinica ukatha pa 30 April.
Kalata yomwe mlembi wa FAM Alfred Gunda walemba yatsindika za chikonzerochi
FAM yati izamukumbukira Marinica popanga mbiri komanso kubweletsa chimwemwe pamene Malawi inafika koyamba mu Round of 16 ku AFCON imene inaseweledwa ku Cameroon chaka chatha.
Usiku wathawu akuluakulu a Malawi Council for Sports ndi a Football Association of Malawi anali mkachipinda komwe amakambirana za tsogolo la mphunzitsi wamkulu wa timu ya dziko lino, Mario Marinica.
Mwa zina amaunikira momwe Marinica wachitira ndi Flames ndipo amvana zoti mgwilizano wake ukafika kumapeto pa 30 April mwezi wa mawa sakuyenera kupatsidwanso mgwilizano wa tsopano.
Choncho lero Football Association of Malawi ikumana ndi mphunzitsiyu kuti amudziwitse izi kuti akhoza kudikilabe kufika pa 30 April kapena atuliletu pansi udindo chifukwa sapasidwanso kontrakiti ina.
The Football Association of Malawi has disclosed that the match between Malawi and Egypt grossed MK76.4 million in gate revenue.
Bungwe lomwe limayang'anira mpira la FAM lanena kuti iwunikila bwino m'mene mphunzitsi wa Malawi wachitira kontrakiti yake ikatha pa 5 April.
A Marinica adasankhidwa kukhala mphunzitsi wa Malawi chaka chatha ndipo adasayina kotrakiti ya chaka chimodzi.
Izi zikudza pamene pali maganizo a anthu osiyanasiyana kuti mwina mphunzitsiyi apasidwe kontrakiti ina kapena ayi kutsatira kusachita bwino kwa Flames mu ndime yozigulira malo mu AFCON.
A Marinica poyankhila pankhani yakusachita bwino kwa Flames ati satula pansi udindo kufikira kontrakiti yawo itatha.