Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"NDAKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati wakhutira ndi zotsatira zomwe timu yake yapeza pomwe yafanana mphamvu 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Chitowe loweruka.
Gondwe anati timu yake inayesesa mpaka kupeza chigoli nthawi yothaitha ndipo akukhulupilira kuti akhale akuchita bwino mu masewero apatsogolo pawo.
"Anali masewero ovuta tithokoze Mulungu kuti tapeza point imodzi. Anzathuwa anachinya patali kwambiri ndipo zimaoneka ngati zitivuta koma sitinatope, tinayesetsa mpaka tinapeza chigoli kutatsala mphindi zitatu." Anatero Gondwe.
Timu ya MAFCO tsopano ili pa nambala 11 ndi point imodzi yomwe ayipeza atasewera masewero awiri mu ligi.
"TAKONZEKA MMENE TIMACHITIRA NTHAWI ZONSE" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati timu yake yakonzeka mmene imachitira pa masewero aliwonse ndipo alibe phuma lopambana masewero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Kamuzu Barracks loweruka ndipo wati iwo asewera mmene amachitira nthawi zonse.
"Takonzekera mmene timapangira nthawi zonse anyamata alibwino ndipo mawa agwira ntchito. Chipambano amapereka ndi Mulungu nde masewero angoyamba kumene tilibe phuma lililonse." Anatero Gondwe.
Timuyi inayamba ligi ya chaka chino moipa pomwe inagonja 2-1 ndi asilikali anzawo a Moyale Barracks sabata yatha.
MAFCO BLAMES OFFICIATION AFTER MOYALE LOSS
MAFCO head coach, Stereo Gondwe, said officiation favours Moyale Barracks in their game and has said the display of the referees was not professional.
Gondwe said this after his team lost 2-1 to Moyale at the Mzuzu Stadium and said bad officiation is destroy Football and making it unprofessional.
"The game was very good. We played very well and controlled thing then we got a goal in the first half but come in the second half the officiation was bad and with this officiation we can not play football, it's bad and it dirtying our Football. I don't talk about referees but it's bad." Said Gondwe.
Following the loss, MAFCO sit 14th in the table as they have a no point in the log table.
๐ท: Aluso media
NEWS
MAFCO FC has announced that they have welcomed back their Head Coach, Prichard Mwansa, who was on holiday since January.
In a press release dated 22 March 2024, confirmed the coming back of the coach who was announced that he has gone to Moyale Barracks two months ago.
"We hereby inform all stakeholders that the coach is back in Salima after his holiday which commenced on January 8, 2024." Reads the final part of the release.
The coach guided the team to two cup finals and league survival on the very last day of the 2023 TNM Super League.
#๐๐ก๐๐ฉ๐ก๐ฎ๐ง๐ณ๐ข๐ซ๐ข๐๐ฐ๐
MWANSA WABWELERA KU MAFCO
Timu ya MAFCO yalengeza zoti mphunzitsi wawo, Prichard Mwansa wabweleraso kutimuyi ndipo atsogolera timuyi ngati mphuzitsi wamkulu mu 2024.
Mmodzi mwa akuluakulu atimuyi, Godfrey Makawano, watsimikiza kuti Mwansa wachoka ku Moyale pomwe wabwerera kuti akapitilize pomwe anasiyira chaka chatha.
Iye wati MAFCO inayamba kale zokonzekera masabata apitawo ndipo akonza kuti chaka chino atengekonso chikho chimodzi.
KAFUNDA SASEWERA KWA CHAKA CHIMODZI
Bungwe la Football Association of Malawi lapereka chilango kwa osewera watimu ya MAFCO, Innocent Kafunda, kuti asasewere mpira kwa chaka chimodzi kamba komenya oyimbira.
Malingana ndi bungweli, osewerayu anaputa othandizira oyimbira pomulozaloza kenako anamenya oyimbira wapanja pa masewero omwe anagonja 1-0 ndi MAFCO mu chikho cha Castel Challenge.
FAM yaperekanso chilango kwatimu yake cha ndalama yokwana K500,000 kamba kokanika kuletsa osewerayu pa mchitidwe wakewu.
"KUPULUMUKA KWAKE KOMA KOVUTA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati phuma lomwe anali nalo tsopano latha kamba koti apulumuka mu ligi koma wati ntchito yake sinali yophweka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Blue Eagles 2-1 koyenda kuti atsalebe mu ligi ndipo wati ntchito ilipo chaka cha mawa kuti akonze timu yabwino.
"Phuma linali ndi ine koma apa latha kwatsala ndi koti chaka cha mawa tipange timu yabwino chifukwa MAFCO ndi timu yabwino ili ndi zoyenereza zonse zabwino nde sitikuyenera kumakhala malo ngati omwe tinaliwa. Mmasewero a lero sizinali zophweka poti Blue Eagles ndi timunso yabwino koma anyamata anamvera kwambiri lero." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yamaliza ligi ndi mapointsi 37 pa masewero 30 omwe yasewera ndipo ili pa nambala 10 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"LIGI YA CHAKA CHINO INALI YOVUTA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati ligi ya chaka chino ya TNM inali yovuta kwambiri pomwe wati matimu omwe ali abwino avutika kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Moyale Barracks pa bwalo la Mzuzu ndipo wati masewerowa anali ovuta kwambiri komabe kutenga point imodzi koyenda ndi zowathandizabe.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse tili kumunsi komanso ndi Red Card yomwe tinapeza mwina inatisokonezabe pang'ono koma point ndi yambiri koyenda kungoti mmene tilili sitimayenera kukhala malo omwe tili, timu ndi yabwino koma zotsatira zikuvuta." Anatero Mwansa.
Iye wati ayesetsa kuti akonze mofooka monse kuti akamadzakumana ndi Blue Eagles adzachite bwino. Timuyi ili pa nambala 12 ndi mapointsi 34 pa masewero 29 omwe yasewera mu ligiyi.
KASONGA WATSOGOLERA MAFCO KUSWA MONACO
Katswiri wa timu ya MAFCO, Peter Kasonga, wagoletsa zigoli zisanu (5) ndipo Mphatso Philimon wamwetsa zitatu ndi zigoli zina za Dan Chimbalanga, Kingsley Nkhonjera komanso David Daudi zathandiza timuyi kufika mu ndime yamatimu 32 amu chikho cha Castel Challenge Cup atagonjetsa Mtengenji Monaco 11-0 pa bwalo la Civo masana a lachiwiri.
Kasonga anatsogoza MAFCO pa mphindi zinayi asanabwerenso pa mphindi 8 kuti masewero akhale 2-0 ndipo anathandizira chigoli cha Dan Chimbalanga pa mphindi 24 komanso Mphatso Philimon anamwetsa chake choyamba pa mphindi 25.
Kasonga anagoletsa chake chachitatu pa mphindi 27 pomwe Kingsley Nkhonjera anagoletsa pa mphindi 34 ndipo Kasonga yemweyo anagoletsanso pa mphindi zoonjezera mchigawo choyamba.
Mtengenji inalimba mchigawo chachiwiri komabe Philimon anaika pa 8-0 pa mphindi 56 asanabwere David Daudi pa mphindi 73, Kasonga anamwetsa chigoli chake chachisanu pa mphindi 89 ndipo Philimon anamaliza mu mphindi zoonjez
MAFCO YAFIKA MU NDIME YAMATIMU ANAYI MU AIRTEL TOP 8
Timu ya MAFCO yakhala yoyamba kuzigulira malo amu ndime ya matimu anayi amu chikho cha Airtel Top 8 kutsatira kulepherana 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks koma iwo apitilira kamba kogoletsa koyenda.
Dan Chimbalanga anamwetsa pa mphindi yoyamba yeniyeni koma Olson Kanjira anabwenza pa mphindi zinayi kuti masewero athere 1-1 zomwe zinasangalatsa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti KB nayo inasewera bwino kwambiri koma tiyamike anyamata poti anachita zimene tinawauza zilibwino kuti tafika mu ndimeyi yomwe ndi yovuta kuti tikadutse koma chanzeru ndi choti tapitilira." Anatero Mwansa.
Timuyi tsopano idikilira matimu ena atatu omwe awatsatire mu ndimeyi ndipo imodzi idziwika lamulungu pomwe Blue Eagles ikulandira Moyale Barracks pa Nankhaka ndipo masewero ali 1-1.
"LERO TIMASEWERA NDI ANTHU 14" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati ngati oyimbira aziyimbira ngati mmene anachitira mmene amakumana ndi Karonga United siziziyenda bwino ndipo wati wawapweteka.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Karonga United pa bwalo la Karonga ndipo wati vuto lomwe lakula ndi loti pali chimene chikusintha akadandaula za oyimbira nde angozitaya.
"Kunena zoona atolankhani mumaona oyimbira athuwa ngati zizitero nde siziziyenda bwino. ziganizo zonse zinali zokondera enawa mwina titha kuti tasewera ndi anthu 14 komabe poti palibe chimene chikumachitika basi tibwerera kwathu." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe yapeza mapointsi 32 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
"SI IFE OKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu yake siyokhutira ndi kufanana mphamvu ndi Silver Strikers pomwe amafunikira chipambano ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 pa Chitowe ndipo wati akonza mavuto awo pomwe akukakunana ndi timu ya Karonga pa bwalo lamulungu likudzali.
"Sife okhutira ndi zotsatirazi, timayenera kupambana chifukwa ndi mmene ligi yavutiramu mapointsi atatu ndi ofunikira koma tatenga imodzi basi tingovomereza." Anatero Mwansa.
Iye wati masewero awo ndi Karonga akhala ovuta kamba koti akakumananso ndi timu yabwino koma ayesetsa kukonza mavuto awo ngati kuphonya Kwambiri kuti akapambane masewerowa.
Timu ya MAFCO ili pa nambala 9 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 32 pa masewero 25 ndipo yatsala ndi masewero asanu kuti amalize mu ligi ya TNM.
"TIVOMEREZE KUTI LERO SITINALI BWINO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu yake sinasewere bwino mmasewero awo a ndime yotsiriza ya FDH Bank Cup mpake akanika kutenga ukatswiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo iye wavomereza za kugonja kwawo mmasewerowa.
"Ife tagonja, sitinachite bwino ndivomereze ngati mphunzitsi kuti zinthu zativuta kuyambirira timakanika kumaka nde anzathuwa anatengerapo mwayi ndi kutichinya nde tiwayamikire poti apambana." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yathera pa nambala yachiwiri ya mpikisanowu pomwe Bullets yamaliza poyamba ndipo yatenga K30 million.
"MAFCO TSOPANO ILI BWINO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO FC, Pritchard Mwansa, wayamikira osewera atimuyi kamba ka kuzipereka kwawo kuti kukuthandiza timuyi kuchita bwino kwambiri mmasewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 ndi Ekwendeni Hammers ndipo wati tsopano timu ya MAFCO ili bwino kwambiri.
"Ndife wosangalala kamba ka chipambanochi, anali masewero ofunikira kwambiri poti ligi yavuta pa log table koma anyamata akuchita bwino, mmasewero 5 apitawa tachita bwino mwina ndi mmene ligi ilili sizophweka kupambana masewero 4-5 nde tiwathokoze." Mwansa anafotokoza.
Timuyi yachoka pa nambala 12 ndipo yafika pa nambala 8 ndi mapointsi 31 pa masewero 24 omwe iyo yasewera mu ligiyi.
"CHIPAMBANO CHINALI CHOFUNIKIRA KWA IFE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati chipambano cha timuyi chinali chofunikira kwambiri kuti aziyendabe bwino kugonjetsa timu ya Civo United 2-0 pa bwalo la Chitowe lachitatu lathali.
Stain Malata anamwetsa zigoli ziwiri mmasewerowa zomwe zathandiza timuyi kupambana ndipo Mwansa wati Civo inasewera mpira wapamwamba koma zigoli za changu zawathandiza kuti apambane.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa Civo yamenya bwino kwambiri komabe anyamata anayesetsa kutsekatseka monse kuti isadutse ndipo zigoli za changu zatithandiza kwambiri, timafunikira kuti tiwine ndithu kuti chitsogolo chikhale chowala." Anatero Mwansa.
Kutsatira kupambanaku, timu ya MAFCO yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 24 pa masewero 21 omwe yasewera. Masewero awo otsatira aliko lamulungu likudzali pa bwalo lomweli ndi Dedza Dynamos.
"ATITULUTSA NDI IWOWO KOMA SITINATULUKE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati anthu omwe akuti timuyi yatuluka kale mu ligi ya TNM akuyankhulira mmaganizo awo koma timuyi ikhalabe mu ligiyi.
Mwansa amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe timu yawo ikumane ndi Civo United pa bwalo la Chitowe ndipo wati timuyi ikuyenera kupeza chipambano mwa njira ina iliyonse.
"Akhala masewero ovuta kwambiri koma tikuyenera kuti tichite bwino chifukwa choti sitili pabwino, tili kumunsi nde chipambano chitithandiza kuti tifike kumtundaku. Ife mu ligi sitinatuluke, awo akuyankhulawo ndi maganizo awo koma adzayankhule ligi ikadzatha." Watero Mwansa.
Timuyi ili pa nambala 14 mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero 20 omwe yasewera. Akapambana, timuyi ifike pa nambala 12 ndi mapointsi 24.
"TITHOKOZE OYIMBIRA AWATHANDIZA A WANDERERS" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu ya Wanderers yawagonjetsa lamulungu chifukwa cha thandizo la oyimbira yemwe ziganizo zake zinakondera timuyi.
Mwansa amayankhula izi atatha masewero ndi timuyi ndipo Wanderers inapambana 1-0 ndi chigoli cha Gaddie Chirwa. Iye wati ndi zoonadi kuti matimu ena akumathandizidwa ndi oyimbira.
"Tithokoze oyimbira kuti wathandiza timu ya Wanderers kuti ipambane chifukwa ziganizo zonse zimakomera anzathuwa, ndivomereze kuti oyimbira ena akumasankhadi matimu oti awathandize nde lero zimene amafuna zachitika, kugwira mu box osayimba ayi." Anatero Mwansa.
Mmasewerowa, katswiri wa MAFCO, Ernest Tambe, anaonetsedwa chikalata chofiira ndipo osewera okwana asanu ndi awiri analandira makalata achikasu. Kutsatira kugonjaku, MAFCO ili pa nambala 14 ndi mapointsi 18 pa masewero 19.
Mafco,
The Malawi Armed Forces College (MAFCO) Football Club have sacked their coach Stereo Gondwe after a dismal start to the season.
The club has since appointed Gondwe's assistant, Ladwell Mbetewa as caretaker for the team.
Since the league started the Salima based club has won one game and lost two consecutive games.
Standard Bank Plc has unveiled a K18.29 million sponsorship for Malawi Armed Forces College (Mafco) football club for the 2023/24 TNM Super League season which kicks off this Saturday.
According to a statement, the sponsorship caters for the teamโs football kit and game allowances in the course of 2023/24 league fixtures.