Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
CHITIPA THANKS KARONGA FOR JOINT FORCES
Chitipa United head coach, Christopher Nyambose, has thanked his fellow Northern region team, Karonga United, for fighting for them in order to stay and said that has shown that they are one.
He said this after the team's 1-3 win over Baka City on the final day at the Karonga Stadium while Karonga United escaped a defeat in Mulanje when FOMO missed an 82nd minute penalty kick to play a 0-0 draw in favour of the Basongo.
Speaking after the game, Nyambose said it could have been a mockery if his team was relegated in the League and has remembered to thank Karonga United for fighting for them.
"We were afraid not because of Baka City but because other teams were playing at their home ground so the result in Mulanje has saved us, we thank Karonga United for the result, they have really shown that we are one." Said Nyambose.
Chitipa United have finished the league with 29 points from 30 points holding a better goal difference than FOMO FC while B
NYAMBOSE ASKS FANS TO STOP BOOING PLAYERS
Chitipa United head coach, Christopher Nyambose, says his team's poor performance in some matches in their home matches is sometimes due to booing of fans on players which gives them pressure when playing.
He said this on Wednesday after the game which they beat Moyale Barracks 2-0 to stay in contention for the survival of the League this season.
He said his team's did not play well in the first half of the game because their supporters were booing them and because most of them are youngsters, they fail to withstand the pressure.
He said, "I think it is not good for fans to be booing the players, they need to encourage the players and not to boo them so today at least better but on Sunday we ask them to stop that."
The Basongo are 15th on the table with ,25 points, two points behind 13th placed FOMO FC and have played 29 matches.
š·: Chitipa United media
Yafika, koma chonde mudziyesetsa kachangu. ZIKOMO
"CHITIPA IS GOING NOWHERE" - NYAMBOSE
Chitipa United head coach, Christopher Nyambose, says his team will not be relegated in the TNM Super League and next season they will play in the top flight as their final two games are at Karonga United which makes them confident to get all 6 points.
He said this after his team's 1-0 defeat over his former club, Mighty Tigers, and said his team could have won the game in the first half but missed a lot of chances.
He said his team is not going anywhere this season and that next season we will be seen in the League.
"Chitipa United is not going anywhere, our two games we are playing at home against Moyale Barracks and Chitipa United and we will fight to get 6 points and reach 29 points then we will see who teaches those points on the final day." Said Nyambose.
The team is still on position 15 on the log table with 23 points from 28 games in the League, four points behind 13th placed Bangwe All Stars.
0991509953 tumizani pa nanba imenei
CHITIPA IKUYANG'ANIZANA NDI KHOMO LOTULUKA MU LIGI
Timu ya Chitipa United ikuchepetsabe mwayi wawo wotsala mu ligi ya TNM pomwe yagonja pakwawo 1-3 ndi timu ya Mzuzu City Hammers very pa masewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Karonga lamulungu masana.
Promise Ogboaza anatsogoza Hammers pa mphindi 28 asanabwere Chimwemwe Chunga pa mphindi 44 koma Ramadan Ntafu anabwenza chimodzi pa mphindi 51 ndipo Gregory Mwase anagoletsa chigoli chachitatu pa mphindi 86 kuti Hammers iweruke bwino.
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake sinasewere bwino mmasewero awo zomwe zinapangitsa kuti akanike kupambana pa masewero awo.
"Anali masewero ovuta kwambiri, tinawapatsa ulemu anzathuwa poti mwina ndi anzathu akumpoto kuno komanso odziwana nawo nde timayesa kuti sabwera mwamphamvu koma masewero alero nde sitinasewere bwino." Anatero Nyambose.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe ili ndi mapointsi 19 pa masewero 25 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
"MPIRA UTHA KUMUPHA MUNTHU NDITHU" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati zomwe waziona tsiku la lero sanazionepo ndipo zikhonza kupha munthu pomwe goloboyi wawo walakwitsa kawiri kuti Mighty Mukuru Wanderers ipambana 1-2 ndi timu yake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anali pa bwalo la Karonga ndipo wati masewero awa ndi opweteka poti angowapatsa a Wanderers zigoli.
"Ndi zopweteka kwambiri ndipo mpira utha kuphadi munthu chifukwa zomwe zachitika panopa sinnazione chifukwa lero nde tataya masewero owinawina komabe goloboyi poti ndikoyamba kugwirira Supa ligi timanjenje koma zapweteka kwambiri." Anatero Nyambose.
Iye wati masewerowa akanathandiza timuyi kuti ifike pa nambala 13 mu ligi koma zateremu zavuta komabe wati chaka cha mawa adzakhala akuphunzitsabe timuyi mu ligi yomweyi.
Iwo akadali pa nambala 15 mu ligi pomwe ali ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligi.
"PADAKALI PANO KULEPHERANA SIKUKUFUNIKIRA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, watsimikizabe kuti timu yake sikutuluka mu ligi koma wapepesa kwa ochemerera atimuyi kuti asapse mtima ngakhale kuti zinthu sizikuyenda padakali panopa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anagoletsetsa chigoli pa mphindi 95 kuti akanike kugonjetsa Premier Bet Dedza Dynamos mmasewero omwe athera 2-2 ndipo wati mmene zililimu, zikufunika kuti azipambana.
"Tiwayamikire kuti anyamata asewera bwino zinangovuta ndi nzeru kumapetoku komabe tinali pakhomo timayenera kupambana chifukwa panopa ligi yavuta tikufunikira kuti tizipambana osati kufanana mphamvu poti ligi yavuta iyi." Anatero Nyambose.
Iye anati pa masewero asanu ndi awiri omwe atsala nawo mu ligi, ayesetsa kukonza zinthu kuti mwina ayembirenso kuchita bwino ndi kusatuluka mu ligi.
Timuyi tsopano yafika pa nambala 14 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 19 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
"KB IDUTSA MOFEWA CHIFUKWA AMENYA KALE NDI YOVUTA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wafunira zabwino timu ya Kamuzu Barracks mu mpikisano wa Airtel Top 8 ndipo akukhulupilira kuti kwinako adutsa mofewa poti ovuta anali iwowo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-3 pa mapenate pomwe mu mphindi 90 anagonja 2-0 koma anafanana mphamvu 2-2 poti anapambana mmasewero oyambawo.
Iye anati, "Anali masewero abwino mapenate amapita kwa wina aliyense koma tiwayamikire a KB asewera bwino ndipo tiwafunire zabwino kungoti achita bwino afika patali poti amasewera ndi timu yovuta lero anawa ayi." Anatero Nyambose.
Iye anati anyamata ake anangogona pang'ono zomwe zinachititsa kuti apezetse zigoli zonse ndipo akakonza mavuto onse kuti achite bwino.
Zateremu, Kamuzu Barracks ikakumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ina ya mpikisanowu pomwe mmasewero ena, Silver Strikers ikukana ndi Mighty Mukuru Wanderers.
CHITIPA YAKHUTIRA NDI POINT IMODZI
Timu ya Chitipa United yati ndi yokhutira ndi kupeza point imodzi koyenda yomwe iwathandizire kuphatikiza pomwe iwo ali napo kale pomwe alepherana 1-1 ndi timu ya Karonga United.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu, Gift Mkamanga, ndi yemwe amayankhula atatha masewerowa ndipo wati timu yake inavutika chifukwa ndi koyamba chaka chino kusewera pa bwalo la Rumphi komabe ndi okondwa.
"Anali masewero abwino kwambiri tinayesetsa kuti tichite bwino ndipo tiwayamikire anyamata chifukwa asewera malingana ndi mmene tinawauzira kuti ngati sitipambana koma tichokeko ndi point nde ndine osangalala." Anatero Mkamanga.
Mmasewerowa, Blessings Mwalilino ndi yemwe anayamba kugoletsa patatha mphindi zisanu ndi imodzi koma Ramadan Ntafu anabwenza pa mphindi 45 kudzera pa penate.
Timu ya Chitipa yakanika kuti ituluke mchigwa cha matimu otuluka pomwe ikadali pa nambala 15 ndi mapointsi 18 pa masewero 22 omwe yasewera.
"KULIKONSE ATITENGEREKO TIKAWACHAPA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati akayambira pomwe anasiyira mu masewero omwe akumane ndi Karonga United kaya pa bwalo lililonse lomwe matimuwa asewerere.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Rumphi ndipo wati amayembekezera kuti akakumana pa bwalo la Karonga komabe kulikonseko iwo akasewera.
Iye wati timu yake ndiyomwe ikufunikira mapointsi kwambiri kuposa Karonga United ndipo akayesetsa kuti akachita bwino.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri, tikayambira pomwe tinasiyira ndipo tikayesetsa kuti tikachite bwino chifukwa tikufunikira mapointsi ndi ife kwambiri kuposa anzathuwa." Anatero Nyambose.
Iye watsindikanso kuti timu yake situluka mu ligi poti ali ndi masewero okwana asanu ndi awiri (7) ndipo palibe kutaya mapointsi mpaka asewera mu Airtel Top 8.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 21 omwe yasewera.
"KOMA KWATHU NDE TIKUCHAPANI MUKABWERA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United wati anthu ayiwale kuti timu yake ituluka mu ligi poti ili ndi masewero asanu ndi atatu apakhomo komwe matimu onse akachokako akulira.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-2 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake ili ndi mpata waukulu wokhalabe mu ligi.
"Tsogolo lilipo lowala kwambiri ndipo chaka cha mawa tisewera mu top 8 mudzandifunse mudzandikhulupilira, ndili ndi masewero 8 pakwathu nde pamene paja palibe angandisunthe ndi tchetchatchetcha basi, tizivutika tikayenda chonchi koma kwathu palibe." Anatero Nyambose.
Timuyi ili pa nambala 14 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino.
Chitipa yapambana kanayi, kufanana mphamvu kasanu ndi kugonja kakhumi ndi kawiri (12) ndipo yagoletsa zigoli 22 ndi kumwetsetsa 34.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr š·: MMH photography
Tumizilani ku 0897788997
"CHIGAWO CHACHIWIRI ASEWERA NDI MA DOTOLO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wadandaula kuti mchigawo chachiwiri cha masewero awo, mpira unayima kwambiri pomwe madotolo amangokhalira kulowa mu bwalo kuti athandize osewera a Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya KB pa bwalo la Nankhaka lachinayi masana ndipo wayamikira anzawowa kamba kokwanitsa kuwagonjetsa.
"Anali masewero abwino kwambiri tinayamba bwino koma timadziwa kuti anzathuwa abwera molimba kwa Ife chifukwa tawagonjetsako kawiri motsogozana nde tiwayamikire kuti achita bwino." Anatero Nyambose.
Iye anati timuyi inakwanitsa kusewera mu chigawo choyamba ndi anzawowa pomwe mchigawo chachiwiri kunachuluka kumenyera mpira panja komanso kugwaigwa.
Timuyi yataya mwayi wotuluka ku chigwa cha matimu omwe akhonza kutuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 20 omwe yasewera.
"KUPANDA KUGONA PA 1-0 POMPAJA TINAYIMALIZA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake inakwanitsa kuchita mmene inakonzeka kuti igwetse timu ya Silver Strikers koma kulakwitsa pang'ono kwachititsa kuchinyitsa chigoli.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi Silver pa bwalo la Karonga lachinayi ndipotu wayamikira osewera ake kamba kosewera bwino mmasewero awo.
"Anali masewero ovuta kwambiri koma anyamata asewera bwino kwambiri, mmene tinakonzera zinatheka ndithu ndipo tikanayimaliza pa 1-0 pomwe paja koma tinagona pang'ono, anaponya mpira uja wina kusumba komabe anyamata asewera bwino." Anatero Nyambose.
Iye wati timuyi itati yatuluka mu ligi ndekuti apha Boma la Chitipa lonse ndipo agwirizana kuti azitolera mapointsi kamba koti mchigawo choyamba anataya kwambiri.
Timuyi ikadali pa nambala 13 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 17 pa masewero 18 omwe iyo yasewera mu ligi ya TNM.
Mabakers
"ENA ATI NDIFE 4 BY 4, TIMASEWERA NDI GOLOBOYI WA MAFCO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati sanali odabwa kuona kuti Christopher Mikuwa anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba pa masewero awo poti timu yawo imasewera ndi iyeyo.
Nyambose amayankhula atatha masewero omwe timuyi yafanana mphamvu 0-0 ndi MAFCO ndipo wati amadziwa kuti MAFCO ibwera movuta poti iwo akumagawa zigoli zinayi.
"Sizodandaulitsa taonjezera point imodzi pamenepo tiwayamikire anyamata asewera mpira wathu changovuta kuti tigwetseremo koma timadziwa kuti MAFCO sibwera mophweka chifukwa ena akumatitcha Mr 4, ena 4 by 4 chifukwa tikumagawa zigoli zinayi nde iwo anali kale akudziwa." Anatero Nyambose.
Iye wati timu yake ikadalipo mpaka kale ndipo chaka cha mawa iseweranso mu ligi ya TNM chifukwa situluka.
Chitipa ikadali pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi okwana 16 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi.
"KWAKWANA NDIPO MATIMU TIWALIZA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake yakonza zolimbikira mmasewero apakhomo ndi cholinga choti azitolera mapointsi omwe akumavuta kuwapeza akayenda.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 4-0 ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Karonga ndipo wachenjeza matimu kuti amva kuwawa akayiyendera timuyi.
"Aliyense akudziwa kuti pomwe tili paja sipakutiyenera nde tikufuna kukhaulitss matimu omwe azibwera pa kwathu poti tikayenda mapointsi akumavuta nde tiwachenjeze matimu kuti amva zowawa zomwe ife timamva tikaluza." Anatero Nyambose.
Iye wayamikira katswiri wawo Trouble Kajani ndi goloboyi wawo watsopano kuti asewera ngati anali kale mutimuyi ndipo akuyembekezera zambiri kuchokera kwa iwo.
Chitipa tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi 15 pa masewero 17 omwe yasewera.
"ALIYENSE AKUMVA KUWAWA NDI POMWE TILI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati anthu onse ku Chitipa United akumva kuwawa ndi pomwe ali ndipo agwirizana kuthandizana cholinga choti achite bwino mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Civil Service United loweruka pa bwalo la Civo ndipo wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta koma ayesetsa kuti chigawo chachiwirichi azitolera mapointsi.
"Akhala masewero ovuta kwambiri, mchigawo choyamba tinavutika kwambiri ndipo Civil iyi inatipanganso chipongwe nde tikudziwa akhale ovuta koma tikufuna kuti tizitolera mapointsi angakhale koyenda kuti tichoke komwe tili chifukwa aliyense zikumupweteka kuti tili kumunsi." Anatero Nyambose.
Chitipa United yatsala ndi mapointsi atatu okha kuti ituluke mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 12 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi.
Vitalite Malawi, a company that provides solar energy solutions to off-grid communities in Malawi is Chitipa United FCās official kit sponsor.
The sponsorship package, unveiled during a ceremony on Monday, 5th August 2024 at Fwasa Lodge in Chitipa, includes essential gear to elevate the team's performance and morale.
The sponsorship includes 32 away jerseys, 32 home jerseys, and various essential gear worth K9 million.
Business Development and Risk Coordinator at the company, Samson Makutu, said their aim to promote their brand within Chitipa District and surrounding areas using the visibility of the team.
In his remarks, Teka Sichera, the team's vice-chairperson, expressed gratitude, noting that the sponsorship will boost morale as the team approaches the second round of the TNM Super League.
1-0
"ANYAMATA ASEWERA MMENE NDIKUFUNIRA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati ndi wosangalala ndi mmene timu yake yasewera ndi Mzuzu City Hammers ngakhale Iwo agonja mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake inavutika kuti tipeze chigoli zomwe ndi ntchito yokha yomwe atsala nayo kuti akonze.
"Ndine wokondwa kwambiri poti lero tasewera bwino kwambiri ndipo ndi mmene timu ya Chitipa ndikufuna kuti izisewerera nde zangotivuta ndi zigoli koma angakhale anzathuwa angopezerapo mwayi kuti goloboyi wathu anakanika kugwira mpira koma sanasewere bwino." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ikadali ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ali pa nambala 14 mu ligi ndi mapointsi okwana 9 pa masewero 14.
JUST IN:
Timu ya Chitipa United yanyamuka pamodzi ndi osewera wawo wakale, Lorenzo Ghedo yemwe tsopano akufuna akayambe moyo watsopano kumeneku kamba koti nthawi yosewera yachepa ku Bangwe All Stars.
Owinna yapeza kuti osewerayu akhale akumalizitsa zapa pepala kudzera mwa omwe amawayang'anira kuti akatumikire timuyi mu chigawo chachiwiri cha 2024.
Lorenzo anali kale kutimuyi mu 2023 pomwe anapita pangongole kuchokera ku Dedza Dynamos komwe anachita bwino ndipo anathandiza timuyi kuthera pa nambala yachinayi mu ligi.
Osewera angapo tsopano achoka kutimu ya Bangwe All Stars kamba kosowa nthawi yosewera ndipo akusaka matimu ena kuti atumikiremo.
"TIMASEWERA NDI WANDERERS YABWINO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake yakanika kupeza chipambano pamwamba pa timu ya Mighty Mukuru Wanderers kamba koti Manoma anali bwino kuposa iwowo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake sinachite bwino makamaka mchigawo choyamba ndipo Wanderers inapezerapo mwayi ndikugoletsa zigoli.
"Tagonja zoonadi timasewera ndi timu yoti inali bwino kwambiri ifeyo timatsalira pa mpira komanso pena timachedwa kumaka mpira zomwe zinapangitsa a Wanderers kuti apeze zigoli zawo koma ifeyo tasewera bwino ndipo timuyi poti tikuyimanga tiyesetsa kuti tikonze zinthu kutimuyi." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 14 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 9 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligiyi.