Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
JUST IN
The Inspector General of the Malawi Police Service, Merlyne Yolamu, has commanded that the prize money for the FDH Bank Cup should be shared amongst the players and the technical panel.
The team has gotten K35 million for winning the trophy on Sunday when they beat FCB Nyasa Big Bullets 3-2 on post match penalties.
📷: MH photography
WANDERERS CONGRATULATES BLUE EAGLES
Mighty Mukuru Wanderers has congratulated Chipiku Stores Central Region Football League side, Blue Eagles for winning the FDH Bank Cup.
The team has written the congratulatory message via their Facebook page after the Area 30 based side managed to beat their City arch rivals, FCB Nyasa Big Bullets 3-2 on penalties after a goalless draw in the 90 minutes.
"The President, Board of Directors, Management and the entire Mighty Mukuru Wanderers FC family, would like to congratulate Blue Eagles FC for winning the 2024 edition of the FDH Bank Cup.
We join the Inspector General and the entire Malawi Police Service in celebrating this achievement together with all football lovers in this country." Wrote the team.
BLUE EAGLES CUP WIN DELIGHTS CRFA
The Central Region Football Association says it is happy to see one of their teams, Blue Eagles, lifting the 2024 FDH Bank Cup and this speaks the volume of their League.
The was said at the Bingu National Stadium where the Area 30 based side were crowned the Champions after beating FCB Nyasa Big Bullets 3-2 on post match penalties following a goalless draw in the 90 minutes.
The Association's general secretary, Antonio Manda, said as an Association, they are happy with Blue Eagles.
He said: "I am excited that team from our region has made history of being first regional team to win national cup in the country. They defeated Silver Strikers, Karonga United, Baka City and now defending Champions, this speaks volume of our league and if we had enough money obviously it would be more than competitive regional league in the country," Said Manda.
Eagles are second in their group in the Chipiku Stores Central Region Football League with 21 points from
BLUE EAGLES YATI ZIKATERE AMAPAMBANA NDI IWO
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake ili ndi mwayi waukulu wotenga chikho cha FDH Bank kamba koti akakumana ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ndime yotsiriza amapambana ndi iwo komabe sazitengera chizolowezi kuopa kupwetekedwa.
Iye amayankhula patsogolo pa ndime yotsiriza ya chikhochi pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe ndipo wati timu yake yapanga zokonzekera zamphamvu kuti tichite bwino.
"Takonzekera bwino kwambiri, tinene kuti tinayamba kukonzekera pakanthawi nde timu ilibwino ndipo ikupereka Chiyembekezo kuti titha kukachita bwino. Linali khumbo lathu kuti tifike mu ndime imeneyi nde lero tafika tithokoze Mulungu chifukwa chokwanilitsa zokhumba nde tikufunitsitsabe titatenga chikhochi." Anatero Kananji.
Iye anati timu yake ili ndi mkwiyo waukulu kamba koti akusewera mu chikho cha Chipiku Stores mchigawo chapakati ndipo uthenga wawo aziupereka mu njira yopambana masewero kuti abwerenso mu ligi.
Timu ya Blue
Blue eagles vs Bullets
"TAKONZEKA KUKUMANA NDI KARONGA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake yakonzeka bwino kukumana ndi Karonga United mmasewero amu ndime yamatimu anayi mu mpikisano wa FDH Bank loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Civo ndipo wati wayesetsa kuwauza osewera ake kulimbikira masewerowa komatu sikuti akhala masewero ophweka.
"Sikuti akhala masewero ophweka chifukwa Karonga United yapano ikusiyana ndi timu yammbuyomu. Iyiyi ikusewera bwino kwambiri zomwe zipangitse kuti tivutike koma tipita ndi mtima wolimbika kuti tikwanilitse khumbo lawo." Anatero Kananji.
Iye wati timuyi yachoka kutali mu mpikisanowu ndipo kufikira pano, maso awo akuyang'ana zogwira chikhochi.
Timu imene idzapambane pa masewero amenewa idzagula malo mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu ndipo adzakumana ndi opambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Moyale Barracks.
"ANYAMATA ATHU ASEWERA BWINO KWAMBIRI" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Eliya Kananji, wathokoza anyamata ake kuti asewera bwino kwambiri zomwe zawathandizira kuti afike mu ndime ina ya chikho cha FDH Bank.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Silver Strikers 5-3 pa mapenate masewero atatha 0-0 mu mphindi 90 ndipo wati timu yake yachita bwino kwambiri.
"Tithokoze Mulungu chifukwa choti tasewera ndi Silver Strikers ndipo tithokoze osewera athu kuti asewera bwino kwambiri tinawauza kuti alimbikire poti anatitulutsa mu ndime ya matimu asanu ndi atatu mu chikho chomwechi chaka chatha nde tibwenze, zathekadi." Anatero Kananji.
Timuyi tsopano yafika mu ndime ya matimu khumi asanu ndi imodzi (16) ndipo ndi timu yachiwiri kuchokera ku ligi yaing'ono kugonjetsa timu yamu Supa ligi.
Mutumizile ku 0994182173
"IFEYO SI PA MPUNGA PA SILVER" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yawo ifunitsitsa itafika patali mwinanso nkutenga chikho cha FDH Bank ndipo anthu asayiphweketse poti ali ku Chipiku.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Silver Strikers mu ndime ya matimu 32 amu chikhochi ndipo wati iwowa sipampunga pa Silver kamba koti akadali ndi mphamvu.
"Akakhala masewero ovuta kwambiri poti ndi amu chikho nde timu iliyonse imakhala yokonzeka kuti ichite bwino, poti tikumenya ku Chipiku anthu asatichepetse ifeyo tikuyang'ana kuti tikachite bwino koma ndi masewero ovuta kwambiri." Anatero Kananji.
Iye anati timu yawo sinagonjeko mu ligi yawo komanso mu zikho zina zimene asewera pomwenso Silver Strikers sinagonjeko mu TNM Supa ligi zomwe zivutitse masewerowa.
Timu imene ingagonje mmasewerowa omwe adzaseweredwe pa bwalo la Nankhaka udzatulukira mu mpikisanowu ndipo wopambana adzapitilira.
📷: Blue Eagles media
"KUKHALA CHETEKO NDEKUTI TIKUFUFUZA" - BANDA
Mlembi wamkulu wabungwe la Super League of Malawi, Williams Banda, wayankhulapo pa kudandaula kwa timu ya Blue Eagles kuti bungweli silikuyankhabe pa dandaulo lawo chifukwa choti likufufuza.
Banda wayankhula izi kutsatira kudandaula kwa Blue Eagles kuti SULOM ikuchedwa kuwayankha koma iye wati angakhale Blue Eagles yomweyo ikudziwa malamulo okhudza nthawi yomwe bungwe lawo likhonza kuwayankhira.
"Dandaulo likafika ndekuti limapita Ku disciplinary komiti yomwe imayenera kuti ifufuze nde kuchedwako sikuti angokhala koma akufufuza. Zokhudza kuti tiyankha liti pali malamulo omwe angakhale a Blue Eagles akuwadziwa komanso inunso mukuwadziwa." Anatero Banda.
Blue Eagles inalembera SULOM kuti ifufuze zachinyengo pakati pa matimu achisilikali a Red Lions komanso Moyale Barracks omwe anathandizira kuti Blue Eagles ituluke mu ligi ya TNM.
"KODI ZIKUFUNIKA KUTI MAKOCHI TIZIKALOWA M'BWALO?" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wadandaula kuti timu yake inangopereka zigoli pomwe tsopano timuyi yatuluka mu chikho cha Castel atagonja 4-2 ndi Silver Strikers.
Kananji amayankhula atatha masewerowa ndipo wati sakudziwano kuti osewera aziwayankhula motani chifukwa akumachita zosiyana ndi zomwe akuuzidwa ngakhale timu yawo ikumasewera bwino.
"Tivomereze tagonja 4-2 ndi timu ya Silver Strikers, chibwana chimalanda olo mutatenga CR Socials zigoli zomwe tachititsa lero sangachinyitse, tangopereka zigoli nde zikumadabwitsa kuti mwina tizikalowa makochi m'bwalomo chifukwa kuwauza sindikudziwa kuti akuganiza bwanji akumapanga zina." Anatero Kananji.
Zateremu timuyi tsopano yamaliza chaka cha 2023 ndipo ayamba kukonzera umoyo wawo mu ligi yaying'ono ya Chipiku Stores ya chigawo chapakati atatuluka mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"TIKUYANG'ANA CASTEL NDIPO AMENEYU TIMWA NDITHU" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya 'Carlsberg Cup' Kananji, wati timu ya Blue Eagles sipita mophweka pomwe akukumana ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Castel ndipo wati timu yonse ikuyang'ana pa chikho chomwechi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Bingu lachitatu ndipo wati timu ya Silver Strikers isapite moderera kuti iwo anatuluka kamba koti apita ndi mtima onse.
"Ndi masewero ovuta kwambiri ndipo anzathuwo asabwere mophweka kuti mwina poti tinatuluka mu ligi koma kukubwera January anyamata akufunikira ka ndalama koti atuluke nako nde ife maso athu ali pamenepa Castel ameneyu timwa ndithu." Anatero Kananji.
Iye wati anyamata ake anachivomera zoti atuluka mu ligi ndipo onse chidwi chili pa masewero amenewa. Omwe apambane mmasewero amenewa adzakumana ndi Bangwe All Stars mu ndime ya matimu anayi.
BLUE EAGLES IKUFUNA KUSUMIRA MOYALE NDI RED LIONS
Timu ya Blue Eagles kudzera mwa wapampando wawo, Alexander Simenti, ikulingalira zokasumira matimu a Moyale Barracks komanso Red Lions kamba koti ali ndi umboni kuti pa masewero awo panachitika zachinyengo.
Iye amayankhula izi ndi nyuzipepala ya Nation kutsatira kutuluka mu ligi kamba koti Moyale Barracks inatenga mapointsi ambiri pamwamba pa iwo poti anafanana chilichonse pa ndandanda wa matimu.
Blue Eagles inapita mu tsiku lomalizali ili pa nambala 9 koma inagonja 2-1 ndi MAFCO pomwe Moyale Barracks inagonjetsa Red Lions yomwe inali itatuluka kale 7-0 zomwe ambiri akayikira kuti anapatsana poti onse ndi asilikali.
Eagles yauza mkulu woyang'ana za milandu kuti akamang'ale ndi kuti Moyale Barracks ipatsidwe chilango ndi kutulutsidwanso mu ligi.
BLUE EAGLES YATULUKA MU LIGI
Timu ya Blue Eagles yatuluka mu ligi yaikulu ya mdziko muno ya TNM Supa ligi pomwe bungwe la Super League of Malawi latengera yemwe anapeza mapointsi ambiri pa mzake kutsatira kufanana chilichonse ndi timu ya Moyale Barracks.
Blue Eagles inapita mmasewerowa ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) koma yagonja 2-1 ndi timu ya MAFCO yomwe nayonso inali pa chiopsezo choti itha kutulukanso ndipo Christopher Sibale wati masewero anali ovuta basi.
"Simmene amayenera kukhalira kungoti anali masewero ovuta kwambiri chifukwa anzathuwa nawonso anali pa ngozi komanso kuti anyamata omwe timayembekezera kuti asintha zinthu sanatero nde sizinayende ndi plan yathu." Anatero Sibale asakudziwa kuti atuluka.
Timu ya Moyale yagonjetsa Red Lions 7-0 kuti afanane ma points ndi zigoli ndi Blue Eagles koma Moyale inapambana ndi kufanana mphamvu pa masewero omwe matimuwa anakumana.
Iyo yatsatira Extreme FC komanso Red Lions ku matimu omwe atuluka mu ligi ya chaka cha 2023.
"BLUE EAGLES NDI MAFCO ILI NGATI NDIME YOTSIRIZA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyembekeza kuti masewero awo ndi timu ya MAFCO lamulungu pa bwalo la Nankhaka akhale ovuta kwambiri poti matimu onse ali ndi zolinga ndi masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pomaliza ligi ya chaka chino ndipo wati akufunitsitsa kupambana ndi cholinga choti asewere nawo mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Airtel Top 8 a chaka cha mawa.
"Kukonzekera kwathu kwayenda bwino ndipo tachilimika chifukwa tikukakumana ndi MAFCO yomwe timavutitsana nayo nde masewero ake akhala ngati a ndime yotsiriza komabe kusewera kwake ndi komwe taonetsa kumapetoku, kungoika mtima kuti chaka cha mawa tidzasewere mu Airtel Top 8." Anatero Kananji.
Timuyi ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 ndipo kupambana ndi MAFCO kutha kudzawatengera pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7).
"KB IMATITENGA NGATI AZIKAZAWO NDE TINATOPA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inakonzeka bwino kwambiri patsogolo pa masewero awo ndi Kamuzu Barracks ndipo anayeneradi kuti apambane.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa KB 3-1 pa bwalo la Civo lachinayi ndipo wati timuyi inatopa kugonja ndi timuyi ndipo apa inabwera ndi mtima wonse kuti ipambane.
"Tithokoze Mulungu komanso tithokoze anyamata athu kamba koti tachita bwino, KB imatitenga ngati azikazi awo tikakumana amangotimenya koma apa tinangoti mmene tinamenyera ndi Bullets tikapite chomwecho nde tinakonzekadi ndipo anyamata achita kunenadi kuti tawathamangitsa." Anatero Kananji.
Blue Eagles yakhala timu yachisanu ndi chiwiri (7) kuti ifike mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Castel Challenge Cup ndipo idzakumana ndi timu ya Silver Strikers mu ndimeyi.
"TIKAKUMANA AMAKHALA MASEWERO OSANGALATSA" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati akuyembekeza masewero apamwamba kwambiri ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati matimuwa akakumana amakhala masewero osangalatsa.
Iye amayankhula patsogolo pa kukumana kwa matimuwa pa bwalo la Bingu mu ndine ya matimu anayi amu chikho cha Airtel Top 8 ndipo wati akonzekera bwino masewerowa.
"Akhala masewero osangalatsa komanso ovuta kwambiri chifukwa tikakumana ndi anzathuwa amakhala masewero ovuta kwambiri komabe ndi masewero aku chikho ndi wofunika kukalimbikira kuti tikafike mu ndime yotsiriza." Anatero Sibale.
Matimuwa anakumananso mu ndime yotsiriza ya chikhochi mu chaka cha 2018 pomwe Blue Eagles inapambana 1-0 kuti atenge chikhochi ndipo mangawa amenewo akadalipobe kumbali ya Bullets.
"BWENZI TIKUTI BLUE EAGLES YAPEZA 3 POINTS" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inasewera mwapamwamba moti ikanatha kupambana mmasewero omwe yalepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets koma mipata yomwe anayipeza aphonya.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 0-0 pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zolakwika zonse akonza kuti mmasewero awo ndi MAFCO adzapambane.
"Tiyamike Mulungu kuti takumana ndi anzathu a Nyasa Big Bullets, tithokozenso anyamata athu asewera bwino kwambiri mwina zangochitika koma bwenzi tikuti Blue Eagles yatenga 3 points koma tikonza molakwika kuti ndi MAFCO tidzapambane." Anatero Kananji.
Kutsatira zotsatirazi, Blue Eagles yasuntha mu ligi ya TNM pomwe tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 35 pa masewero 29 mu ligiyi.
"TIKANGOMENYA EXTREME BASI TIDZAKUMANA 2024" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati masewero omwe timu yake ikukumana ndi Extreme FC loweruka akhala ovuta kwambiri koma chipambano ndi chofunikira kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Nankhaka ndipo wati akapambana masewero amenewa, akhala kuti apulumuka basi.
"Ndi masewero ovuta kwambiri poti anzathuwa zatsimikizika kuti tsopano atuluka mu ligi nde alibe phuma lililonse zomwe zivutitse masewerowa komabe tawauza anyamata kuti kupambana titseka zoyankhula zonse tikapanda kutero atiyikadi mmagulu aja omati tili pa chiopsezo chotuluka koma kungopambana basi tidzakumana mu 2024." Anatero Kananji.
Blue Eagles ili pa nambala 10 mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 31 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
"TINANGOYIWERENGA MU ZOFOOKA ZAWO" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati kutenga point imodzi pamwamba pa Chitipa United ndi yofunikira kamba koti iwasuntha ndi mmene ligi yavutiramu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Karonga lolemba ndipo wati iwo anagwiritsa ntchito kuiona malo omwe akufooka kuti apeze zigoli zawo.
"Tinaona momwe akufooka nchifukwa chake tinapeza chigoli mwa changu kwambiri ndipo kumapeto tinawaona kuti atopa nde tinatenga ena ammbali kuti apite pakati kuti tichulukepo mpake tinapeza chigoli chobwenzera chija." Anatero Sibale.
Kutsatira kupeza point imeneyi, Eagles yasuntha kufika pa nambala 11 ndi mapointsi 31 pa masewero 26 omwe yasewera.
#KasongaJr
ZILANGO KU SULOM ZAYAMBA POMWE EAGLES YALANDIRA
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu mdziko muno ya Super League of Malawi lapereka chilango kwa osewera anayi a timu ya Blue Eagles komanso wothandizira mphunzitsi watimuyi, Christopher Sibale, kamba koyambitsa zisokonezo pomwe ankasewera ndi Ekwendeni Hammers ku Mzuzu.
Mu kalata imene bungweli latulutsa lolemba lapereka chilango kwa kwa osewera atimuyi monga Sankhani Mkandawire, Tonic Viyuyi, Chakonda Majanga komanso Ranken Mwale kuti apereke K500,000 kamba kofuna kumenya oyimbira ndipo Mwale amupatsa chilango chosasewera masewero anayi.
Sibale naye alipira ndalama yokwana K500,000 kamba kochita nkhalidwe loyipa ndipo Blue Eagles ilipira ndalama zokwana K1.5 million kamba kokanika kuteteza anthu awo.
Ndalamayo ikuyenera kuperekedwa pasanathe masiku 14 ndipo pa mlanduwu, Blue Eagles inathamangitsa oyimbira kamba kosakhutira ndi kayimbilidwe mmasewero omwe anagonja 1-0 ndi Ekwendeni Hammers.