MARK HARISSON ALI PA MPENI
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Mark Harrison ali ndi tsogolo la pendapenda kutimuyi pomwe walephera kupambana mmasewero oyamba pa atatu omwe anapatsidwa kuti apambane.
Owinna ikudziwa zoti Harrison anapatsidwa masewero atatu amu Supa ligi kuti apambane atagonja mmasewero awo ndi Extreme FC. Mmasewero oyamba, Wanderers yafanana mphamvu ndi Dedza Dynamos 1-1 ndipo otsatira awiriwo akumane ndi FCB Nyasa Big Bullets ndi MAFCO.
Zinthu sizikuyenda kutimuku pomwe ochemerera atimuyi anayendetsa wapansi osewera ndipo ena anamenyedwa atatha masewero awo ndi Dedza Dynamos.
They must fire him quickly