"OYIMBIRA AKU MALAWI ATHA KUMAYIMBIRA MIPIKISANO IKULUIKULU" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wapereka chiyembekezo kuti oyimbira a mdziko muno akhonza kumayimbira mipikisano yaikulu ngati African Cup of Nations ndi CHAN poti zonse zili mchimake.
Iye amayankhula pa mwambo wopereka zitupa kwa oyimbira omwe bungwe la FIFA lawavomereza ku hotela ya Sunbird Livingstonia ku Salima lamulungu masana.
Iye wayamikira oyimbira kuti ayimbira bwino mu chaka cha 2024 pomwe zoliralira zinachepa kwambiri mu chakachi ndipo wati tsopano oyimbira akuno atha kumakayimbirano mipikisano ikuluikulu.
Iye anati: "Chimene chimavuta ndi choti oyimbira athu anali asanakhale ndi maphunziro a VAR koma apa tsopano aphunzira mwayi umenewu ukhonza kutseguka."
Oyimbira 16 ndi omwe apatsidwa zitupa za FIFA ndipo asanu ndi oyimbira apakati, asanu ndi anayi ndi othandizira ndipo awiri ndi oyimbira masewero apagombe.
Khumi ndi awiri ndi aamuna pomwe anayi ndi amayi ndipo Mayamiko Kanjere, David Chinoko, Sibusiso Sibande ndi Solomon Siliwonde ndi omwe apatsidwa chitupachi posachedwapa.
Tumizilani pa 0981511741
Mutumizile pa 0981511741
tumizilani ku 0981511741
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores