FAZILI WATENGA OSEWERA ANAYI KU U-20
Mphunzitsi wa Scorchers, Lovemore Fazili, watenga osewera anayi omwe anasewera nawo ndi timu ya osewera osapitilira zaka 20 pa ndandanda wa osewera omwe akupita nawo ku mpikisano wa COSAFA.
Anayiwa omwe ndi Olivia Phikani, Sarah Mlimbika, Leticia Chinyamula ndi Maureen Kenneth atengedwa kamba kusewera bwino pomwe anakwapula Guinea Bissau 5-1 pa bwalo la Bingu.
Mphunzitsiyu watenga osewera 24 omwe akayimilire dzikoli ku mpikisano omwe uyambe pa 18 February mpaka pa 1 March.
Osewera monga Vanessa Cikupila,Β Tendai SaniΒ ndi Chisomo Banda ndi omwe amasewera kunja kwa dziko lino omwe atengedwa.
Ndandanda onse ndi uwu:
PAGOLO Mercy Sikelo (Kukoma Ntopwa) Yamikani Kaonga (MDF Lioness) Esther Maulidi (Wanderers Queens)
KUMBUYO Chimwemwe Madise (TP Mazembe) Ireen Khumalo (Silver ladies) Rose Alufandika (Kukoma Ntopwa) Maggie Chavula (Ascent) Maureen Kenneth (Ascent) Doreen Dickson (MDF Lioness) Benadetta Mkandawire (Bullets Women)
0984871619
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores