Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Silver 2-0 Bullets
Bullets 2 : silver 1 full time
BB2 1 SILVER
Bullets all the way
BULLETS IKUMANA NDI SILVER LOWERUKA
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Silver Strikers akumana mu ndime yotsiriza ya chikho cha Airtel Top 8 kutsatira kupambana masewero awo amu ndime ya matimu anayi a mpikisanowu.
Timu ya Bullets inagonjetsa Kamuzu Barracks 2-0 pa masewero omwe anaseweredwa lamulungu pa bwalo la Bingu ndi zigoli za Ephraim Kondowe komanso Blessings Mpokera.
Ndipo timu ya Silver Strikers inadalira chigoli cha Binwell Katinji kuti igonjetse Mighty Mukuru Wanderers 1-0 loweruka kuti ikhale yoyamba kufika mu ndimeyi.
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti ndime yotsirizayi iseweredwe loweruka pa 09 November 2024 pa bwalo la Bingu lomweli nthawi ya 3 koloko masana.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Ikanakhalaso ya 5pm
2-2 in 90min
FC Nyasa 2-1 Kamuzu Barracks
Who is red carded
Manoma forever 😍
Power 🏁
Airtel top 8 fixtures