NKHANI
Katswiri wakale wa Flames, Chimango Kayira, walengeza kuti wapita Ku timu ya Ntaja United komwe akakhale ngati wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu Mavuto Lungu.
Iye watsimikiza yekha za nkhaniyi pa tsamba lake la mchezo la Facebook.
Kayira wati wathokoza timuyi pomukhulupilira ndipo akuyembekeza kuphunzira zambiri kwa Lungu komanso kuthandiza timuyi ndi ukadaulo wake.
Iye wapita ku timuyi patangodutsa sabata imodzi atalengeza Kuti watula pansi ngati mphunzitsi wamkulu watimu ya Liberty.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores