Timu ya Ekhaya yalengeza kuti yasaina katswiri wotchinga pagolo, Clever Nkungula, kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets.
Katswiriyu yemwe wakhala ali wovulala kwa nthawi ndithu tsopano alibwino ndipo ali wokonzeka kugwira ntchito pansi pa Enos Chatama yemwenso anali mphunzitsi wake ku Bullets Reserve.
Iye wakhala ku Bullets kwa zaka 7 pofikira chaka chino pomwe amachokako.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores