"Tiyesa kukamba nawo a TNM" - Gangata
Nduna ya zamasewero mdziko muno, Alfred Gangata, ayamikira kampani ya TNM pothandiza ligi yaikulu mdziko muno ponena kuti athandiza kutukula mpira wamiyendo mdziko muno.
Iwo amayankhula lachinayi pa mwambo omwe kampaniyi imapereka mphoto kwa osewera, olemba nkhani, oyimbira ndi matimu omwe achita bwino mu ligi ya chaka cha 2025.
TNM tsopano sizithandizanso ligiyi kutsatira kuti SULOM inapeza FDH Bank ngati othandiza atsopano ndipo Gangata wati ayesa kukamba nawo kuti asachokeretu ku maseweroku.
"Tiwathokoze poti athandizs kutukula masewero ampira. Tiyesa kukamba nawo ngati angathandizebe zinthu zina," iye anatero.
TNM inayamba kuthandiza masewero a mpira mu chaka cha 2006 ndipo akhala kwa zaka 18.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores