"POINT IMODZI KOYENDA NDI YABWINO" - KADZUWA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, McNerbert Kadzuwa, wati timu yake yakanika yokha kupambana masewero awo komabe wati kutenga point imodzi asangalala.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Dedza Dynamos 0-0 ndipo wati anyamata ake asewera bwino kwambiri ndipo anangokanika kupeza chigoli.
"Anali masewero abwino ndipo tasewera bwino kwambiri koma kungoti mwayi wopeza chigoli sunapezeke komabe sizinayipe chifukwa kupeza point imodzi kuyenda sizophweka nditha kunena kuti tasangalala." Anatero Kadzuwa.
Iye watinso kutolera mapointsi asanu pa masewero asanu ndi awiri omwe asewera sizinayipe kwambiri poti mapointsi akuvuta kwambiri mu ligi ndipo wathokoza anyamata ake poti akugwira ntchito yabwino.
Chitipa United ili pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) pomwe ali ndi mapointsi asanu (5) pa masewero asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores