CRFA YAYAMBA KUFUFUZA ZACHINYENGO KU LIGI YA CHIPIKU
Bungwe la Central Region Football Association layimitsa kaye masewero otsiriza pakati pa Namitete Zitha komanso Kawinga FC pomwe pakumveka kuti panachitika zachinyengo pakati pa matimuwa.
Lamulungu lathali, Namitete imayenera kukumana ndi Ngolowindo mu ligiyi ndipo amafunitsitsa kuti akagoletse zigoli zambiri kuti mmasewero awo otsiriza ntchito idzachepeko koma Ngolowindo sinabwere pa bwalo.
Timuyi inakamang'ala pa nkhaniyi ndipo pabwera maumboni oonetsa kuti timu ya Kawinga inakapereka ndalama ku Ngolowindo kuti asapite ndipo kuti Namitete ilandira zigoli ziwiri basi.
Bungweli lifotokoza tsatanetsatane wa nkhaniyi mmasiku akudzawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores