MAYERE A NDIME YA MATIMU ANAYI A CASTEL ALIKO LERO
Bungwe la Football Association of Malawi lichititsa mayere a ndime ya matimu anayi amu chikho cha Castel pomwe matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Moyale Barracks akhale akupumulira pa masewero awo pa bwalo la Kamuzu lero.
Bungweli lalengeza za nkhaniyi kummawaku ndipo matimu omwe akhudzidwe ndi Bangwe All Stars yomwe yafika kale mu ndimeyi, wopambana pakati pa Blue Eagles ndi Silver Strikers, Wopambana pakati pa Mighty Mukuru Wanderers ndi Moyale Barracks komanso wopambana pakati pa Ekwendeni Hammers komanso FCB Nyasa Big Bullets.
Ichi ndi chaka choyamba chikhochi kuseweredwa mu dziko lino ndipo matimu odutsa 2000 ndi omwe asewera nawo mu mpikisanowu. Awa ndi omwe akhudzidwe mu mayerewa.
1. Bangwe All Stars 2. Mighty Mukuru Wanderers | Moyale Barracks 3. Ekwendeni Hammers | FCB Nyasa Big Bullets 4. Silver Strikers | Blue Eagles
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores