EAGLES YATENGA BONONGWE
Timu ya Blue Eagles yasaina katswiri otchinga pagolo ku timu ya Chintheche United, Justin Bonongwe, pa mgwirizano wa zaka zitatu.
Bonongwe yemwe amaseweranso masewero apa gombe omwe timati Beach Soccer, wasaina mgwirizanowu ndi ndalama yokwana K1 million kwacha.
Iye wapita kutimuyi pomwe akukalowa mmalo mwa Brighton Munthali yemwe anapita ku Black Leopards yaku South Africa komanso John Soko yemwe ali ku maphunziro aupolisi.
Eagles ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe yakwanitsa kupeza ma pointsi 16 pamasewero 16 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores