BLUE EAGLES YAIMITSA KUWALI
Timu ya Blue Eagles yaimitsa mtsogoleri wa osewera atimuyi, Schumacher Kuwali, kuti asatengepo mbali pa masewero atimuyi kuyambira pano kupita mtsogolo pomwe timuyi yamupeza olakwa popanda ulemu.
Mu kalata yomwe timuyi yatulutsa lachisanu yati katswiriyu anasowa khalidwe pomwe amayankhula mosakhala bwino kwa osewera anzake ndi akuluakulu ena ophunzitsa timuyi.
Timuyi yati katswiriyu asiya ikuoneka kutimuyi kuyambira tsopano ndipo nthawi yodzabwereranso sikudziwika poti adzachita kumuuza.
Masewero oyamba iye osapezekapo ndi omwe timuyi ikusewera ndi Karonga United pa bwalo la Nankhaka lamulungu likudzali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores