WALTER WAPAMWAMBA KU CAF
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, wapambana pa chisankho chaku Confederations of African Football ngati mmodzi wamu komiti yaikulu ya bungweli oyimira kummwera kwa Africa.
Nyamilandu wapambana chisankhochi ndi mavoti 36 kuposa waku Mauritius, Mohammed Ally Samir Sobha yemwe anapeza mavoti 15 komanso waku Lesotho Mokhosi Philip Mahapi yemwe anapeza mavoti anayi (4).
Nyamilandu akhala pa mpando umenewu mpaka mu chaka cha 2027. Iye wagwiraponso ngati mmodzi mwa akuluakulu a khonsolo ya FIFA mmbuyomu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores