"SIZOPHWEKA KUGONJETSA WALTER NYAMILANDU" - MWENDA
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi wakale, James Mwenda, wati si ntchito yophweka kugonjetsa Walter Nyamilandu Manda pa mpando wautsogoleri wa FAM pomwe waonetsa chidwi choimanso pa chisankho cha bungweli mu December.
Mwenda anaimapo pa mpandowu mu 2019 atagwira ngati wachiwiri kwa Nyamilandu kuchokera 2014. Iye wati ali ndi chidwi chodzaima nawo pa mpandowu.
"Ngati anthu omwe amavota ku FAM atandipatse mpata ondisankha, sindidzaganiza kawiri ndipo ndidzaimira." Anatero Mwenda.
Iye anati anamva kuwawa atagonja pa zisankho za mpandowu koma wakonza molakwika monse ngakhale akudziwa kuti akukumana ndi namandwa pa nkhani zamasewero.
"Ndikudziwa ndikukakumana ndi nkhalakale pa nkhani zamasewero, sizophweka kuti umupambane ndipo zikufunika masamu ndi kukonzekera kwapamwamba." Anaonjezera Mwenda.
Iwo adzapikisana ndi Nyamilandu yemwe wakhala pa mpandowu kuchokera mu 2004 mpaka pano.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores