OSEWERA ASANU NDI AWIRI A BULLETS SAPEZEKA NDI WANDERERS
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Callisto Pasuwa wati sakhala ndi anyamata ake asanu ndi awiri (7) pomwe timuyi ikumane ndi Mighty Mukuru Wanderers mu TNM Supa ligi loweruka likudzali.
Pasuwa amayankhula izi ndi olemba nkhani a timuyi patsogolo pa masewerowa ndipo wati Eric Kaonga walowanso mu gulu a osewera ena asanu ndi mmodzi omwe sanapezeke mmasewero a Kamuzu Barracks.
"Eric Kaonga nayenso wavulala ndipo Nickson Nyasulu, Chinedu Okafor ndi Yankho Singo ayamba zokonzekera zofewerako pomwe Mike Mkwate, Clyde Senaji ndi Stanley Biliati akanasowabe kwa masabata angapo kutsogoloku." Anatero Pasuwa.
Timu ya Bullets ili pa nambala yachiwiri mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 21 ndipo ikutsogola ndi mapointsi atatu pamwamba pa Wanderers yomwe ikubwera pachitatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores