KODI SULOM NDI MWANO KAPENA ZIWINDI?
Bungwe la Super league of Malawi (SULOM) laumilirabe kuchititsa masewero a pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu angakhale kuti bungwe la Football Association of Malawi linaletsa masewero ngati awa pa bwaloli.
Bungwe la FAM linayankhulapo kuti cholakwika chidzachitike pa masewerowa chisadzawakhudze ndipo SULOM yati sikusinthabe masewero aliwonse ndipo aseweredwa mmene ayikidwira.
Izi zapereka mafunso ochuluka kwa anthu osiyanasiyana pa mmene mabungwe awiriwa amagwilira pomwe ubale sukuoneka pakati iwo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores