OSEWERA A EXTREME ANASIYA ZOKONZEKERA ATAGWEBA MANOMA
Mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wadandaula ndi mchitidwe wa osewera ake omwe akumazikweza akachita chinthu chapamwamba pomwe akumasiya kuchita zokonzekera za timuyi.
Kafoteka amayankhula izi lamulungu atagonja 1-0 pakhomo ndi Ekwendeni Hammers mu TNM Supa ligi. Iye wati anaona khalidwe lachilendo atagonjetsa Mighty Mukuru Wanderers mmasabata awiri apitawo.
"Ndi zachilendo ndipo sindinazionepo zikuchita angakhale ine ndikusewera mpira kuti kusiya training kamba koti agonjetsa timu yaikulu." Anatero Kafoteka.
Iye walangiza osewerawa kuti asewerere tsogolo lawo mu mpira osati ndalama chifukwa atha osapita patsogolo. Extreme ili pa nambala 16 pomwe ndi pansi penipeni pa ligiyi ndi mapointsi asanu okha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores