CHESTER WAUZA MANOMA KUTI SAKUBWERA POSACHEDWA
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Yamikani Chester, wauza mmodzi mwa ochemerera atimuyi kuti sangabwerere kutimuyi kamba koti ali ku ntchito.
Izi zadza pomwe masapota atimuyi anakhamukira ku tsamba la katswiriyu ati kumupempha kuti abwerere kutimuyi pomwe zotsatira sizikuoneka bwino mu ligi ya chaka chino.
Koma poyankhapo, Chester anauza mmodzi mwa ochemererawa kuti iye sangafike kutimuku pano.
"Ndikanali Kaye ku ntchito bwana." Anatero Chester.
Katswiriyu anachoka kutimuyi kumayambiliro kwa chaka chino pomwe sanamvane ndi timuyi nkhani za mgwirizano wake ndipo iye akutumikira timu ya Costa do Sol yaku Mozambique.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores