MABEDI WAKONDA SINGINI
Mphunzitsi watimu ya Flames, Patrick Mabedi, akuyang'ana zoitana mtsogoleri wa timu ya Ekwendeni Hammers, Blessings Singini, kuti akatumikire mu timuyi ku COSAFA Cup ku South Africa.
Mabedi akufuna katakweyu yemwe wachita bwino kwambiri chaka chino ndi timuyi posewera pakati mmasewero onse omwe timuyi yasewera.
Singini wakhala katswiri wosewera bwino mmasewero awiri chaka chino ndipo mu sabata yangothayi, wagoletsa zigoli zitatu pa masewero awiri ndi Extreme FC komanso Airborne Rangers
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores