FAM NDI SULOM ALI PA MKULIRANO
Bungwe la Football Association of Malawi (FAM) lati cholakwika chilichonse chomwe chidzachitike pa masewero a FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers zisadzawakhudze pomwe bungwe la Super League of Malawi layika masewero pakati pa matimuwa pa bwalo la Kamuzu lowerukali.
Izi zadza pomwe bungwe la FAM linaletsa masewero akuluakulu pa bwaloli poti silili bwino koma SULOM yachita mosemphana ndi zimenezi. Mlembi wamkulu wa bungwe la FAM, Alfred Gunda wati ngati zitavute zisawakhudze.
"Ngati SULOM siyisintha masewerowa ndekuti atiderera nde kalikonse komwe kadzachitike kasadzatikhudze." Anatero Gunda.
Masewero amatimuwa amayenera kuchitikira ku bwalo la Bingu ngati kunali kutsatira mawu a FAM. Pakadali pano SULOM ikuonetsa kuti sikubwenza ganizo lawo lochititsa masewerowa pa bwaloli.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores