Timu ya Mighty Wakawaka Tigers yatuluka mu chikho cha FDH Bank pomwe yagonja 3-1 ndi Santhe Admarc yomwe imasewera mu Chipiku Stores Central Region Premier Division.
Masewerowa anafika ku mapenate pomwe anathera 1-1 ndipo Precious Chipungu anagoletsa pa mphindi 29 ndipo Wellington Mkandawire anazigoletsera yekha mu golo lake.
Ku mapenate, goloboyi wa Santhe Admarc anachotsa ma penate awiri ndipo wati Tigers anachotsa limodzi kupangitsa Santhe kuti ipambane.
Iyo yakhala timu yachikhumi kuzigulira malo mu ndimeyi pomwe FCB Nyasa Big Bullets, Mighty Mukuru Wanderers, Silver Strikers, Extreme FC, Kamuzu Barracks, Moyale Barracks, MAFCO, Balaka FC ndi Bangwe All Stars afika pa ndimeyi.
Santhe won 4 penalties for 2. Why are you writing 3-1?
Ayi anathera 3-1
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores