MPONDA WAPEZA NTCHITO KU SOUTH AFRICA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Mponda walowera mdziko la South Africa komwe akukamalizitsa zokhala mphunzitsi watimu ya Black Leopards ya mdzikomo.
Mponda watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti timu yake yakaleyi inamufikira ndipo sakanakana ayi.
"Takambirana kale chilichonse pakati pa mbali zonse ndipo chatsala ndi kusainirana mgwirizano ndipo zimenezo zitha kuchitika lero." Anatero Mponda.
Timuyi imasewera mu ligi yachiwiri mdzikomo ya Motsepe Foundation Championship ndipo mu ligi yangothayi, timuyi inatuluka koma yagulanso malo amu ligiyi kutimu ya All Stars. Mutimuyi mumasewera osewera ake akale omwe wawaphunzitsa ku Sure stream Academy, Dennis Chembezi ndi Raffick Namwera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores