MADINGA ATHA KUBWERERANSO KU WANDERERS
Mphekesera yakula kuti katswiri wakale wa Mighty Mukuru Wanderers, Francisco Madinga atha kubwerera kutimuyi.
Izi ndi malingana ndi zomwe Owinna yapeza kuti katswiriyu, yemwe wapambana ukatswiri ndi timu ya Jwaneng Galaxy yaku Botswana, akhonza kuonekanso ku Lali Lubani pomwe nthawi yake yosewera ili yochepa kutimuyi.
Lachinayi, mmodzi mwa akuluakulu atimuyi, Samuel Mponda, analemba mozimbayitsa kuti katswiriyu abwerere kutimuyi ndikudzaithandiza komwe zikukaikitsa kuti nkhaniyi itha kukhala yolondola.
Katswiriyu anachoka kutimuyi mu 2020 pomwe anapita ku timu ya Dila Gori FC yaku Georgia ndipo wapita tsopano ku Botswana chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores