OYIMBIRA ATATU APATSIDWA ZILANGO ZOSAYIMBIRA KWA MIYEZI
Oyimbira atatu, Alfred Chilinda, Michael Mwambyale komanso Mark Zrmbaseko sapezeka kwa miyezi ingapo kutsatira kuti komiti ya oyimbira mdziko muno yawapatsa zilango kamba kokanika kuimbira bwino mmasewero amu TNM Supa ligi.
Mlembi wa bungweli, Chris Kalichero watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati Chilinda sayimbira masewero kwamiyezi inayi (4) pamene Mwambyale ndi Zembaseko akhala miyezi isanu ndi umodzi (6) aliyense asakugwira ntchito kamba ka zolakwitsazi.
Chilinda wapezeka olakwa pamlandu wokana chigoli cha Civil Service United komanso kupereka ziganizo zosakhala bwino kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets ponena kuti osewera awo anali offside pomwe matimu awiriwa amakumana mu TNM Super league masabata angapo apitawa pabwalo la Civo mudzinda wa Lilongwe omwe anathera 1-1.
Nawo a Mwambyale komanso Zembaseko analephera kupereka chikalata chofiira kwa Christopher Kumwembe komanso kukanira Tigers chigoli mmasewero awo ndi Wanderers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores