Katswiri wa Scorchers, Sabina Thom, wanyamuka mdziko muno kupita ku Democratic Republic of Congo komwe akukayezedwa za chipatala ndipo zikatheka iye asaina mgwirizano ndi timu ya TP Mazembe.
Thom, yemwe amasewera MDF Lioness mdziko muno, wakhala ofunikira kwambiri kumbali ya timu ya dziko lino pomwe anayithandiza kufika mu ndime yotsiriza ya COSAFA Women's Championship mu chaka cha 2021.
Iye anasainidwapo ndi timu ya Simba SC yaku Tanzania koma anabwereranso mdziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores