Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"IT'S EVERY TEAMS WISH TO WIN THE LEAGUE" - MWASE
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Meke Mwase, says every team including his team wish to win the league this season and that the battle is still on.
He said this after his team failed to trim their gap on Silver Strikers to 6 points after recording a goalless draw at the Dedza Stadium on Sunday afternoon.
Speaking after the match, Mwase said the match was very tough as they played away from home and thanked his boys for trying to secure a win.
After being asked if he is still optimistic about winning this year's league, Mwase said every team wish so.
He said: "It's every team's wish to win the league."
The Nomads are now 8 points adrift leaders, Silver Strikers as they have 32 points from 17 games they have managed to play this season.
Tatumiza ndalama kwa owina nonse 👏
0984000038 tumizilani imeneyi
"GOLOBOYI WATITHANDIZA KWAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wayamikira kwambiri wotchinga pagolo wawo, Donnex Mwakasinga, kuti wawathandiza kwambiri pa masewero omwe amasewera ndi Mighty Mukuru Wanderers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Dedza ndipo wati anali masewero ovuta kwambiri omwe anayesetsa kuti apeze chigoli komabe anakanika.
"Anali masewero ovuta kwambiri, matimu onse anakonzeka kwambiri kuti mwina achite bwino mutha kuona kuti kupeza mipata kumavutanso mmasewero amenewa koma tithokozenso goloboyi wathu watipulumutsa, timayenera kupeza chipambano kutengera ndi pomwe tili koma zativuta." Anatero Bunya.
Iye wati anthu asadere nkhawa kamba koti posachedwa aywmbe kubweretsa zotsatira zabwino pomwe atha masewero anayi osapambanako.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi mapointsi okwana 20 pa masewero 17 omwe yasewera.
Noma win dedza Lose
Fcb win moyale lose
SALIMA, MAPEMBA MISSES OUT ARROWS GAME
FCB Nyasa Big Bullets will not have their two Reserve side graduates, Crispin Mapemba and Chikumbutso Salima, who are injured when they play Red Arrows in the first leg of the CAF Champions League preliminary round match on Sunday.
The team's head coach, Kalisto Pasuwa confirmed about the news ahead of the match at the Bingu National Stadium and said the team's problem again is having many injuries.
"One again we are back into the Champions League, we have been having problems of injuries but there are guys who have been training as you know we registered more than 25 players and from these 25 players we also last week played a league match and we lost Crispin Mapemba and Chikumbutso [Salima] can be doubtful again as doctors say he is not yet okay." Said Pasuwa.
He further said the players available on the day will be used against Red Arrows but in their previous match against Civil Service United, people doubted them but still they made, they
"TITHOKOZE OYIMBIRA AKUKONZA MPIRA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wadandaula ndi mmene oyimbira achitira pa masewero awo ndi timu ya Blue Eagles mu ndime yamatimu anayi a mpikisano wa FDH Bank ponena kuti agonja kamba ka iwo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 kuti atuluke mu chikhochi ndipo wati sangayankhule zambiri poti wawapatsa zigoli a Blue Eagles.
"Anali masewero ovuta kwambiri ndipo timu yathu sinasewere bwino tithokozenso oyimbira powapatsa masewerowa a Blue Eagles akuthandiza kutukula mpira mdziko muno." Anatero Kaunda.
Iye koma wathokoza osewera atimu yake kuti ayesetsa kufika ndimeyi ngakhale ili timu ya Osewera achisodzera ndipo wati chidwi chawo ayika ku ligi ya TNM.
Timuyi tsopano yatuluka mu chikhochi ndipo Blue Eagles ikumana ndi timu yopambana pakati pa timu ya Moyale Barracks komanso FCB Nyasa Big Bullets.
"KWAKWANA NDIPO MATIMU TIWALIZA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wati timu yake yakonza zolimbikira mmasewero apakhomo ndi cholinga choti azitolera mapointsi omwe akumavuta kuwapeza akayenda.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 4-0 ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Karonga ndipo wachenjeza matimu kuti amva kuwawa akayiyendera timuyi.
"Aliyense akudziwa kuti pomwe tili paja sipakutiyenera nde tikufuna kukhaulitss matimu omwe azibwera pa kwathu poti tikayenda mapointsi akumavuta nde tiwachenjeze matimu kuti amva zowawa zomwe ife timamva tikaluza." Anatero Nyambose.
Iye wayamikira katswiri wawo Trouble Kajani ndi goloboyi wawo watsopano kuti asewera ngati anali kale mutimuyi ndipo akuyembekezera zambiri kuchokera kwa iwo.
Chitipa tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi 15 pa masewero 17 omwe yasewera.
"OSEWERA ANATOPA CHIFUKWA BUS INAFA" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati zinali zovuta kuti timu yawo ipeze chipambano poti afika mochedwa ku Karonga kamba koti galimoto yawo yoyendera inaonongeka ku Lilongwe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-0 ndi Chitipa United ndipo wati kuchezera mausiku awiri akuyenda ndi kusapuma zapangitsa iwo kuti asachite bwino osati Kadi yofiira yomwe osewera wawo anapatsidwa.
"Chomwe ndinganene ndi choti zinali zovuta kupambana chifukwa osewera atopa. Galimoto inationongekera pa Lumbadzi tikubwera Juno nde tinathapo tsiku tili pomwepo tinachita kubwereka ina nde tafika mmawa wa lero zinali zovuta." Anatero Yasin.
Iye anati timuyi yapezetsa zigoli zophweka kwambiri ndipo kadi yofiyira yomwe Gabinho Daudi anapatsidwa sangadandaule chifukwa osewera amayenera azikhala ndi khalidwe.
Timuyi tsopano ili pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 12 pa masewero 17 omwe yasewera.
Boa tard?
Wawa?
Zikuti bwanji kumeneko?
Harentals queens
Young Africans
Liverpool
Green buffaloes
"IT'S ANOTHER MATCH! A DIFFICULT ONE" - MWASE
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Meke Mwase, says he is going to employ another tactical approach when they face Premier Bet Dedza Dynamos as they need to treat their opponents differently.
This comes after the Nomads demolished Mzuzu City Hammers 8-0 with a 3-5-2 system and Mwase said he is going to change the approach against Dynamos at the Dedza Stadium on Sunday.
"We are very prepared for the game the boys look very sharp and we are hoping that we will get a win. It's another game that is going to be tough so we need to take it seriously in order for us to win." Said Mwase.
He said a win would be important for the Nomads as they will keep on moving up and closer to Silver Strikers who have opened a wide game on them in the league.
The Nomads have 32 points from 16 games in the TNM Super League and second on the standings.
"CHIPAMBANO CHILI MMAGANIZO ATHU" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati chipambano chikhale chofunikira kwambiri kutimu yawo poti ayamba udyo mu chigawo chachiwiri cha ligi ndipo akufunitsitsa kusunthira kutsogolo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Dedza lamulungu ndipo wati timu yake ikuyenera kuyiwala zoti sanagonjetsepo Wanderers kuti adzachite bwino.
"Kutengera ndi mmene tayambira sizilibwino tinagonja ku Balaka nde tikuyenera kuti tichilimike cholinga tipambane nde anyamata akuoneka alibwino ndipo chipambano ndi chotheka chifukwa tisuntha kwambiri tikapambana." Anatero Bunya.
Iye wati timuyi ikayesetsa kumenyera nkhondo kuti ikapambane ndipo kufika kwa osewera ena kutimuyi monga Dan Mponya ndi Justice Honde kuwathandiza kulimbitsa malo ena mu timuyi.
Dedza ili pa nambala 10 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 16 omwe yasewera mu ligi.
📷: Dedza media
Saint louis
Moyale barracks
Mzuzu city hummers
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati akonzeka kuti achite bwino pamene akuyembekezera kukumana ndi timu ya Mighty Tigers pa bwalo la Mulanje Park loweruka pa August 17.
M'mawu ake mphunzitsiyu wati akudziwa kuti adzakhala masewero ovuta kutengera kuti Tigers ili pakhomo komanso ndi mmene matimu aimira pa ndandanda wa matimu mu ligi.
"Ife takonzekera masewerowa. Mchigawo choyamba tinawina kwathu 1-0 nde tikudziwa kuti masewerowa akhala ovuta kutengera kuti Tigers ndi timu yabwino komanso ndi mmene ligi ilili panopa masewerowa siakhala ophweka koma tiyesetsa kuti tichite bwino," watero Mwansa.
Moyale ikukasewera masewerowa ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) ndi ma points okwana 23 mumasewero 16 ndipo idamwetsa zigoli 17 ndi kumwetsetsa zigoli 14.
Mighty Tigers ili pa nambala 12 ndi mapointsi 15 itamwetsa zigoli 11 ndikumwetsetsa zigoli 23 mu masewero 16 omwe yasewera.
Sabata yatha Moyale idafananitsa mphamvu itachokera kumbuyo m'masewero omwe adatha 1-1
"NDI TSIKU LALIKULU KU KARONGA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati loweruka ndi tsiku lalikulu ku Karonga lomwe anthu amu bomali akuliyembekezera poti lionetsa tsogolo la timuyi mu chikho cha FDH Bank.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Blue Eagles mu ndime ya matimu anayi ndipo wati timuyi yakonza kuti ikapambane koma sizibwera mophweka poti akuyenera kutuluka thukuta.
"Takonzekera bwino kwambiri masewerowa ndipo ili ndi tsiku lalikulu kwa osewera, kwa onse aku Karonga, kwa makolo athu, abale athu ndi ena chifukwa litionetsa tsogolo lathu koma tikufunitsitsa kuti tikapambane koma sizikhala zophweka." Anatero Kaunda.
Iye anatinso timu ya Blue Eagles ili ndi mphunzitsi wabwino yemwe amadziwa ntchito komanso kuti ndi timu yabwino zomwe zitavutitse masewerowa.
Opambana pa masewerowa adzakumana ndi opambana pakati pa matimu a Moyale Barracks komanso FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ina ya matimu anayi.
"TAKONZA KUTI TIKAPAMBANE NDITHU" - IKWANGA
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Kondwa Ikwanga, wati akudziwa kuti akuchoka kogonja mochititsa manyazi ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers 8-0 koma akonza mavuto awo kuti achite bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya FOMO FC omwe aseweredwe pa bwalo la Mzuzu loweruka ndipo wati timu yake yakonza kuti ikachite bwino.
"Tikuchoka kogonja, osatinso kugonja chabe Kona mochititsa manyazi moti anthu amaona kuti palibe chanzeru tikupanga koma titaunguza mavuto takonza ndipo chimene tikuyang'ana ndi chipambano koma zitengera kulimbikira kwa osewera." Anatero Ikwanga.
Iye wathokoza mabwana a timuyi pomulora kuti akonze mavuto awo omwe alipo ndikuwaphunzitsa osewera awo mopanda phuma kusatengera kusachita bwino kwa timuyi.
Hammers sinagonjeko pakhomo pawo chaka chino ndipo ili pa nambala yachinayi ndi mapointsi 25 pa masewero 16 omwe yasewera.
NKOLONGO PROMISES FIRE IN COSAFA TOURNEY
Ascent Academy director and head coach, Thom Nkolongo, says his side is upbeat to kick off the COSAFA CAF Women's Champions League campaign with a win when they play Young Buffaloes from Eswatini on Friday afternoon.
Nkolongo said this ahead of the match saying the team are in the competition not just to participate but to compete and has promised Malawians to record a win in their first match.
"We will fight to secure a win this afternoon as the girls are very ready to showcase what we have been preparing. We are into the tournament not to participate but to compete so we did well in the local tournament and that's where we will start off in this tournament." Said Nkolongo.
This is the first time Ascent Academy is playing in the tournament but second from Ntopwa Super Queens in Malawi after they played in 2023.
The National Champions are in group Because of the tournament alongside UD Lichinga, Young Buffaloes and Gaborone Ladies.
Manchester united 1-2Fulham
"TAKONZEKA KUKUMANA NDI KARONGA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake yakonzeka bwino kukumana ndi Karonga United mmasewero amu ndime yamatimu anayi mu mpikisano wa FDH Bank loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Civo ndipo wati wayesetsa kuwauza osewera ake kulimbikira masewerowa komatu sikuti akhala masewero ophweka.
"Sikuti akhala masewero ophweka chifukwa Karonga United yapano ikusiyana ndi timu yammbuyomu. Iyiyi ikusewera bwino kwambiri zomwe zipangitse kuti tivutike koma tipita ndi mtima wolimbika kuti tikwanilitse khumbo lawo." Anatero Kananji.
Iye wati timuyi yachoka kutali mu mpikisanowu ndipo kufikira pano, maso awo akuyang'ana zogwira chikhochi.
Timu imene idzapambane pa masewero amenewa idzagula malo mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu ndipo adzakumana ndi opambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Moyale Barracks.
Haiya promises more international tournaments hosting
Football Association of Malawi President, Fleetwood Haiya, says he is happy to host the first ever Women's international tournament and has promised to host kinds of these tournaments in his tenure.
Haiya said this after the kick off of the COSAFA CAF Women's Champions League in Malawi at the Mpira Stadium on Thursday afternoon where 8 teams from different countries are meeting in a bid for a ticket to the fourth edition of CAF Women's Champions League.
Haiya said he is happy to host this kind of tournament which will help to expose talents in Malawi and also inspire young girls who also wish to play Football at a higher level to work hard and set goals.
He said if he is to be given 19 years just as the people which his predecessor, Dr Walter Nyamilandu Manda, stayed on the seat, Malawi will host many international tournaments.
He said: "This is not the first tournament to host in my 7 months stay as a president, remember we
had the four Nations tournament which was for men's football so in 7 months, we have had two tournaments, what if I am given 19 years then it will be more so I hope this wouldn't be the last tournament to host."
Meanwhile, the minister of Youth and Sports, Hon. Uchizi Mkandawire thanked the government for their support in the women's football and pledged for more support in different sporting activities and national teams.
He said, "Government is committed in supporting football in all spheres as we are building different stadiums in the country and also we have been supporting national teams in different tournaments so we need to see them performing well and we remain committed to continue helping them."
The tournament started with group A matches as Herentals Queens from Zimbabwe beat FC Ongos Ladies from Namibia 3-1 in an early kick off match whereas 2022 edition Champions, Green Buffaloes from Zambia managed to beat University of Western Cape from South Africa 1-0.
WANDERERS YATI BULLETS NDE YOKUBA OSEWERAYO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yaloza chala timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti ndi imene imaba osewera chifukwa yakhala ikuphumitsidwa osewera awiri mmbuyomu.
Mkulu wa timuyi, Panganeni Ndovi, wati timu ya Bullets inawalanda Lloyd Aaron ndi Chawanangwa Gumbo pomwe Manoma anali atapanga kale gawo lalikulu lokambirana ndi matimu awo.
"Izizi kumpira zimachitika. Mwinanso nkhani ya Promise Kamwendo bola Koma Chawanangwa Gumbo anabwera ku Blantyre kunoko kuti akubwera ku Wanderers." Anatero Ndovi poyankhulana ndi nyuzipepala ya Nation.
Izi zikutuluka pomwe matimuwa atengerana ku Football Association of Malawi pomwe Bullets yati inali itapereka kale ndalama pa katswiri wotchedwa Promise Kamwendo yemwe anakasaina mgwirizano ku Wanderers.
Source: Nation
Flames legend, Chiukepo Msowoya has been roped into Mighty Tigers technical panel as he will be their new Strikers trainer.
He will work with his former teammate, Robert Ng'ambi, who is the assistant coach to Leo Mpulula at the team.
NEBA MAWA ZITHA BWANJI?
Bb vs moyale
TUNDE WINS BULLETS POTM AWARD
Nigerian forward, Babatunde Adepoju, has won the player of the month award at FCB Nyasa Big Bullets after helping the team to secure good results in the month of July.
In the month he described as a month of turning following a slow start on his return, Babatunde managed to score five goals in five games for the People's team and two were against Mighty Mukuru Wanderers in the FDH Bank Cup round of 16.
He has beaten Lloyd Aaron, Nickson Nyasulu and Chikumbutso Salima through votes from supporters to win the award.
Bullets vs moyale
Cosafa club championship
Fdh cup
OFFICIAL: West Ham have completed the signing Aaron Wan-Bissaka from Manchester United! A contract until June 2031. A transfer fee worth £15M.
2-1
Mpira wathu
MAPHUNZIRO A VAR AKUYAMBA LERO
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti maphunziro a oyimbira a masiku asanu a mayiko omwe ali pansi pa bungwe la FIFA akuyambika mtsiku la lero ku Mpira Village ku Blantyre.
Maphunzirowa ayitanitsa oyimbira 35 kuchokera mmadera osiyanasiyana mdziko muno ndipo pamwamba pa maphunzirowa, Iwo aphunziranso kagwiritsidwe ka makina atsopano a kanema omwe amathandizira kuyimbira (Video Assistant Referee)
Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya, analengeza posachedwa kuti makinawa ayamba kugwira ntchito mdziko muno posachedwapa.
MANOMA AVOMERA KULAKWA KWAWO KU FAM
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yavomereza milandu yomwe inapatsidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi kutsatira zachipolowe zomwe timuyi inachita pa masewero omwe inagonja 2-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets mu chikho cha FDH Bank mwezi watha.
Mu kalata yomwe timuyi yalemba ku bungweli lati silikufuna kuvutavuta pa nkhaniyi pomwe yavomereza kulakwa kwawo.
Koma timuyi yati ikamapereka chigamulochi iyang'anenso mmene anachitira powaletsa ochemerera awo kusiya kugenda zomwe zinathandizira kuti masewero apitlirebe.
Timu ina ya Karonga United inalandiranso chosagwiritsa bwalo la Karonga kwa masewero atatu komanso kupereka K1 million kamba ka zachiwawa zomwe anachita pomwe ankasewera ndi Mzuzu City Hammers mwezi watha umwewu.
"CHILANGOCHI NDI CHUMA CHATHU SICHIKUGWIRA" - SIMWAKA
Timu ya Karonga United yati chilango chomwe bungwe la Football Association of Malawi lawapatsa chosasewera masewero atatu pa bwalo lawo ndi chowawa kwambiri kuposa chopereka K1 million poti awononga ndalama zambiri pa masewerowa.
Mlembi wamkulu wa timuyi, Ramzy Simwaka, wati akuluakulu atimuyi akhale akukumana kuti awunikire chilangochi kuti ngati kuli kotheka akasume kuti awachepetsere.
"Mukati muone kukasewera ku Mzuzu ndekuti tiziononga ndalama yokwana K50 million mmasewero amodzi komanso tikakhala pakhomo timatha kupeza ndalama zambiri zapakhomo nde chilangochi chatipweteka kuposa kupereka K1 million." Anatero Simwaka.
Chilangochi chabwera kamba koti ochemerera atimuyi anachita ziwawa pa masewero omwe ankasewera ndi Mzuzu City Hammers mu chikho cha FDH Bank mwezi watha.