Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
RAIPLY ITHA KULANDA MWAYI WA SONGWE BORDER
Nkhondo yolimbilirana malo amu ligi yaikulu ya TNM ikuyenera kufika potentha kwambiri koma wolowa mu ligi adziwike sabata ino kuti ndi Songwe Border United kapena timu ya Raiply FC.
Timu ya Songwe Border inataya mwayi wozigulira malo mu ligiyi pomwe imangofunikira point imodzi koma inagonja 2-0 ndi timu ya Chintheche United lachitatu lapitali.
Izi zatsegula mpaka kutimu ya Raiply FC yomwe ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi 21 pa masewero 12 kuti ngati ipambane masewero awo ndi Chilumba Barracks lowerukali kenako ndi kumenya Songwe Border lamulungu ndekuti atha kulowa mu ligi.
Songwe Border ili ndi mapointsi okwana 27 pa masewero 13 kuti atsala ndi amodzi basi okumana ndi Raiply ndipo achinya zigoli 17 ndi kuchinyitsa 14 pomwe Raiply yachinya 18 ndi kugoletsetsa 10 zokha.
Timu yomwe ilowe mu ligiyi ilowa pamalo pa Baka City yomwe yatuluka kale mu ligiyi ndipo Chitipa United ithanso kutuluka mu ligiyi.