Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"KUCHINYITSA ZITATU ZOKHA PA WANDERERS NDI CHILIMBIKITSO" - MKANDIRA
Mphunzitsi watimu ya Panthers, Innocent Mkandira, wati ndi chilimbikitso chachikulu kwambiri ku timu yawo kungogonjako zigoli zitatu zokha pa masewero omwe anakumana ndi Mighty Mukuru Wanderers poti osewera awo sangafanane ndi a Wanderers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 kuti atuluke mu chikho cha Castel Challenge mu ndime ya matimu anayi ndipo wati iwo anayesetsa koma zavuta.
"Mutha kuona mchigawo choyamba tinayesetsa kuyimitsa Wanderers sitinachinyane koma mchigawo chachiwiri tinakanika kumaka bwinobwino nde atachinya choyamba anatibalalitsa kwambiri." Anatero Mkandira.
Iye wati komabe kutengera kukula Kwa timu ya Wanderers ndi luso la osewera atimuyi alili, kugonja ndi zigoli zitatu zokha ndi chilimbikitso chachikulu kwambiri.
Wanderers yafika mu ndime yotsiriza ndipo ikumana ndi wopambana pakati pa timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi Mzuzu City Hammers.
Nonse takutumizirani ndalama zomwe mwawina 👏👏
CIVIL SLAIN, WANDERERS NEXT AS PANTHERS BOOK LAST FOUR PLACE
The lower league side, Panthers FC have managed to knock out four Elite League giants in a similar way through post match penalties after beating Civil Service United 4-2 on penalties after playing a goalless draw in 90 minutes.
In the shootouts, Only Blessings Malinda and Chifundo Ngapemba scored for Civil as Moses Banda and Festus Duwe missed their kick while Happy Kasamba, Anold Masamba, Vincent Mark and Uchizi Ngulube Scored their kick to move into the last four of the Castel Challenge Cup.
Coach Innocent Mkandira has warned teams coming ahead of them that if they sleep they will see what other teams have seen already.
"I'm happy that we have achieved what we said that we will not give any chance to any Super League team ahead of us so today we have done it again, I am very happy." Said Mkandira.
Meanwhile, he said his team was much motivated when they beat Silver Strikers in the round of 32 of the tournament and tha
PANTHERS IKUYANG'ANA ZOKAFIKA NDIME YOTSIRIZA
Mphunzitsi watimu ya Panthers, Misheck Kachika Jere, wati timu yake yaika maso ake polimbikira kuti mwina ikafike mu ndime yotsiriza ya mpikisano wa Castel pomwe wati zilichonse ndi chotheka mu mpira.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Silver Strikers 3-4 pa mapenate kutsatira kulepherana 2-2 mu mphindi 90 ndipo anali wosangalala kwambiri.
Iye anati timu yake sikuti imachita kukonza kuti izigo matimu akuluakuluwa mu ndime ya mapenate pomwe zimangochitika koma wati akufuna akathere patali.
"Zikupereka chilimbikitso kwambiri kuti tinagonjetsa MAFCO apa tagonjetsa Silver Strikers nde tingolimbikira kuti tifike patali mwina ndime yotsiriza poti chilichonse ndi chotheka mu mpira." Anatero Jere.
Zateremu, timuyi yafika mu ndime ya matimu khumi, asanu ndi imodzi (16) ya mpikisanowu ndipo pakhale mayere kuti timuyi idziwe yemwe adzakumane naye.