Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"KULUZA MASEWERO NDI ZAMPIRA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake inayesetsa kuti ichite bwino ndipo inakonza kuti ipambane mmasewero awo koma sizinayende ndi momwe anakonzera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Bangwe All Stars lamulungu pa bwalo la Balaka ndipo wati timu yake inapeza mipata yochuluka kwambiri yomwe anakanika kugoletsa.
"Anali masewero abwino kwambiri tinapeza mipata kuti mwina tikanatha kupeza zigoli koma tinakanika komabe zimachitika mu mpira tibwerera tikakonze mavuto athu kuti tipitilire kuchita bwino." Anatero Mwansa.
Moyale Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi okwana 36 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Bangwe 1-0
"TIKUYENERA KUKAWINA MWA NJIRA ILIYONSE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake ikuyenera kulembetsa chipambano mwa njira iliyonse pa masewero omwe akumane ndi timu ya Mzuzu City Hammers pa bwalo la Mzuzu loweruka kuti mwina asunthe pa ndandanda wa matimu.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa ndipo wati monga mchigawo choyamba chinatha 1-1, masewerowa akhale ovuta kwambiri potengera kuti matimuwa ndi odziwana koma akayesetsa kuti akachite bwino.
"Ndikukhulupilira kuti akhala masewero ovuta kwambiri chifukwa tikusewera ndi timu yabwino kwambiri komanso tikudziwana koma anyamata akonzeka komanso kuti tikachite bwino tikufunika kukalimbikira nde mwa njira iliyonse tikachita bwino." Anatero Mwansa.
Iye wati timu yake ikuyenera kuti ikagwiritse ntchito pa mimwayi yomwe akapate mu mmasewerowa ndi cholinga choti akakwanitse kupeza zigoli zochuluka pa masewerowa.
Moyale ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi okwana 32 pa
"NDASANGALALA NDI MMENE TASEWERERA MCHIGAWO CHACHIWIRI" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati si zinthu zophweka kugoletsa zigoli zitatu ndi kupambana masewero mu chigawo chachiwiri cha ligi ndipo wati ndiwokondwa ndi mmene timu yake yasewerera mchigawo chachiwiri cha masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya FOMO FC 3-1 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati wasangalala kwambiri ndi chipambanochi.
"Anali masewero abwino kwambiri FOMO ndi timu yabwino ndipo yasewera bwino kwambiri komanso inayamba kugoletsa koma tinabwenza ndipo mchigawo chachiwiri tinawauza anyamata, asewera bwino kwambiri mpaka tapeza zigoli ndasangalala kwambiri." Anatero Mwansa.
Iye wati ayesetsa kuti ngakhale masewero azivuta chotere, timuyi izitolera mapointsi mu ligi kuti athere pabwino ligi ikamadzatha.
Zateremu timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi okwana 32 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligi.
"OYIMBIRA AMBIRI NDI MASAPOTA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wadandaula ndi momwe oyimbira ambiri mdziko muno akuchitira pomwe akumasankha timu yomwe ipambane pa masewero zomwe zikupweteka kwambiri matimuwa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Civil Service United ndipo wati ngakhale kuti iwo anaphonya mipata yochuluka koma oyimbira atengapo mbali kuti agonje zinthu zomwe oyimbira ochuluka akumachita mdziko muno.
"Anali masewero abwino kwambiri tasewera bwino tinapeza mipata yambiri maka mchigawo choyamba koma tinakanika kugoletsa komabe kwa nthawi yoyamba ndiyankhulako za oyimbira,"
"Zomwe akupanga sizabwino ndipo mayimbilidwe awawa mpira sungapite patsogolo, kuchita kukondera mbali imodzi angakhale anthu omwe anaonera ndi pakanema pomwe atha kutsimikiza, ambiriwa ndi masapota." Anatero Mwansa.
Kutsatira kugonjaku, Moyale ili pa nambala 10 mu ligi pomwe ikadali ndi mapointsi okwana 29 pa masewero 22 omwe yasewera.
📷: Civo media
Miyare win
"POINT IMODZI SINANDISANGALATSE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati siokhutira ndi kupeza point imodzi pamwamba pa timu ya Creck Sporting Club ndipo wati iye anakonza kuti timuyi ipambane masewero ake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Mzuzu loweruka masana ndipo wati timu yake sinasewere bwino ngati momwe imadziwikira.
"Anali masewero ovuta kwambiri sitinasewere bwino ngati momwe timasewerera mopatsirana ndi kupita kutsogolo nde kupeza point imodzi sinandisangalatse poti tinakonza kuti tipeze chipambano pa masewerowa koma zavuta." Anatero Mwansa.
Iye wati timu yake ikhale ikukonza mavuto awo omwe awaona mmasewerowa ndipo akakonza akuyembekezera kuti azichitanso bwino mu ligi.
Moyale tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 29 pa masewero 21 omwe iyo yasewera.
"TIKANGOLIMBIKIRA KUTI TIKAPAMBANE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake ikayesetsa kuti ikalimbikire ngati akufunitsitsa chipambano pamwamba pa timu ya Creck Sporting Club masana a loweruka mu ligi ya TNM.
Iyi amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali pa bwalo la Mzuzu ndipo wati mu ligi tsopano mulibe timu yaikulu koma nkhani ikumakhala kulimbikira basi.
"Takonzekera bwino masewerowa kuti tipeze mapointsi onse poti tili pakhomo komanso kuti tisunthepo pa ndandanda wa matimu. Sizingabwere mophweka koma tikalimbikira tichita bwino nkhani panopa ngakhale Bangwe All Stars yamenya Bullets osati kuti ilibwino kapea kuti ichoka kumunsi kuja koma kulimbikira basi." Anatero Mwansa.
Timu ya Moyale Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi okwana 28 pa masewero 20 omwe yasewera.
MOYALE BREAKS BANKERS HOME POINT BOX
Moyale Barracks has become the first team in the 2024 season to leave at Silver Stadium unharmed after forcing Silver Strikers to a 1-1 draw on Saturday afternoon.
Emmanuel Allan scored an opener for the visitors on 23rd minute before Zebron Kalima cancelling out the scores 7 minutes later and an outstanding performance of Olyce Nkhwazi denied the Bankers a winner.
Head coach for the team, Prichard Mwansa, said a point taken away from home is precious but lamented his players for not being clinical upfront.
He said: "It was a good game the boys played very well although it was a tough one but they really fought only that we got good chances which we could have won this match but our finishing part was not good so a point away from home is not bad."
The Kaning'ina Lions are on position 6 with 28 points from 19 games in the League having won 6 games, drawn 10 times and lost 4 times.
POOR OFFICIATION CLAIMS CONTINUE IN CHITOWE
Moyale Barracks has become the latest team in the TNM Super League to speak again unfair officiation at the Chitowe Stadium where MAFCO FC uses as their home after several teams made similar claims before.
The team's head coach, Prichard Mwansa, after a 1-1 draw against MAFCO which Godfrey Nkhakananga was the referee and said this is not good for our Football in the country.
"We should also be worried of the officiation today, it was not good and we have talking about this for several times, this is not good at all." Said Mwansa.
He further said that his team missed a lot of good chances including a penalty miss which made them fail to record a win but an away point is valuable to them.
The team stays 7th on the table with 27 points from 19 games they have played in the 2024 TNM Super League season.
"CHOFUNIKIRA NDI KUWINA OSATI KUPATSIRANA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake sinasewere bwino pamasewero omwe amasewera ndi Karonga United koma chomwe chimafunikira ndi mapointsi atatu basi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anapambana 1-0 loweruka pa bwalo la Mzuzu ndipo anati timu yake imayenera kupambana chifukwa mmasewero awiri apitawo sanakwanitse kuchita bwino.
"Masewero ayenda bwino chifukwa tapambana lero, tinavutika kwambiri tinafanana mphamvu ndi Bullets ndikugonja ndi Tigers nde mapointsi awawa anali ofunikira kuti tipeze pakhomo zomwe zatheka, sitinasewere bwino inde koma chomwe timafuna ndi kupambana basi." Anatero Mwansa.
Timu ya Moyale Barracks yafika pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 26 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
"KUVUTA KWA MAYENDEDWE KWATISOKONEZA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake inachedwa kufika chifukwa choti bus yomwe Iwo amagwiritsa ntchito imakanika kulira ndipo mayendedwe anakonzedwa mochedwa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu mpikisano wa FDH Bank ndipo wati kuchedwaku kwawasokoneza mu zambiri mpake anapezetsa zigoli mwansanga.
"Tikhonza kunena kuti zatisokoneza chifukwa tinangolowa mu bwalo la zamasewero osaziongola mwinanso ndi zomwe zinapangitsa kuchinyitsa zigoli mwa msanga komabe ndisayankhule kwambiri za zimenezo." Anatero Mwansa.
Iye anati tsopano poti timu yake yatuluka mu chikhochi, iwo ayika chidwi chawo mu ligi ya TNM kuti amalizire pabwino ligi ikadzatha.
Katswiri wotchedwa Babatunde Adepoju anagoletsa zigoli ziwiri pomwe Ephraim Kondowe anamwetsa chimodzi ndi Emmanuel Allan anamwetsa chopukutira misonzi kuti masewerowa athere 3-1.
MWANSA WATI AKUKHULUPILIRA KUTI ACHITA BWINO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati akhulupilira kuti timu yake ichita bwino pa masewero amu FDH Bank mu ndime ya matimu anayi malingana ndi mmene timuyi yakonzekerera masewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa awo ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Bingu lachitatu ndipo wati akudziwa kuti akhale masewero ovuta koma akufuna kufika mu ndime yotsiriza.
"Takonzekera bwino kwambiri masewero amenewa tikukhulupilira kuti mmene tapangira anyamata akupereka chilimbikitso kuti tichita bwino ndi kufika ndime ina nde tikayesetsa kuti tikachite bwino." Anatero Mwansa.
Timuyi tsopano ikufunitsitsa kufika mu ndimeyi chifikereni mu 2017 pomwe inasewera ndi Kamuzu Barracks mu chikho cha FISD Challenge ndipo anagonja.
Opambana pa masewero amenewa akuyembekezeka kukumana ndi timu ya Blue Eagles mu ndime yotsiriza.
Wolemba: Hastings Kasonga
FCB 2-0 moyale
Moyale barracks
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati akonzeka kuti achite bwino pamene akuyembekezera kukumana ndi timu ya Mighty Tigers pa bwalo la Mulanje Park loweruka pa August 17.
M'mawu ake mphunzitsiyu wati akudziwa kuti adzakhala masewero ovuta kutengera kuti Tigers ili pakhomo komanso ndi mmene matimu aimira pa ndandanda wa matimu mu ligi.
"Ife takonzekera masewerowa. Mchigawo choyamba tinawina kwathu 1-0 nde tikudziwa kuti masewerowa akhala ovuta kutengera kuti Tigers ndi timu yabwino komanso ndi mmene ligi ilili panopa masewerowa siakhala ophweka koma tiyesetsa kuti tichite bwino," watero Mwansa.
Moyale ikukasewera masewerowa ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) ndi ma points okwana 23 mumasewero 16 ndipo idamwetsa zigoli 17 ndi kumwetsetsa zigoli 14.
Mighty Tigers ili pa nambala 12 ndi mapointsi 15 itamwetsa zigoli 11 ndikumwetsetsa zigoli 23 mu masewero 16 omwe yasewera.
Sabata yatha Moyale idafananitsa mphamvu itachokera kumbuyo m'masewero omwe adatha 1-1
"TAKHUTIRA NDI MMENE TACHITIRA MCHIGAWO CHOYAMBA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati ndiwokondwa poti timu yake yamaliza chigawo choyamba ndi mapointsi abwino ndipo wati alimbikira kuti achite bwino mchigawo chachiwiri cha ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Silver Strikers 0-0 pa bwalo la Mzuzu lamulungu ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri komanso wakondwa ndi mmene achitira.
"Takhutira ndi mmene tachitira mchigawo choyamba, inde panali masewero ena mwina tikanachita bwino koma anyamata analimbikira kuti tikhale pomwe tilipa ndipo kusagonja pa bwalo la Mzuzu zatithandiza kwambiri." Anatero Mwansa.
Iye wati timu yake ikhale ndi mwayi wowonjezera kutsogolo kwawo osewera angapo poti masewero achuluka mu ligi ndi zikho zina.
Moyale ili pa nambala yachisanu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 22 pa masewero 15 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
MOYALE YAKWIYA NDI SULOM
Timu ya Moyale Barracks yalembera kalata bungwe la Super League of Malawi kuti litsatire kusakondera komanso kukonza zinthu ngati momwe amanenera kuti zinthu zawo ziziyenda bwino.
Iwo afunsa bungwe pa nkhani ya kuphwanyidwa kwa bus yawo ndi atimu ya Dedza Dynamos komanso kuti osewera ena anavulazidwa ndipo SULOM sikukakamiza Dynamos pa chigamulo chomwe inapatsidwa kuti ichite.
Pa 20 February chaka chino, SULOM inauza Dynamos kuti ikonzetse bus ya Moyale komanso kulipira pa thandizo lililonse la chipatala la osewera omwe anavulala pa chiwembuchi komatu chichokereni pa 14 October 2023, Dynamos sinalipire komanso SULOM yangoti chete.
Iwo ati akufuna kuti a Dedza Dynamos akonzetse bus yawoyi komanso apereke chipukuta misonzi kwa osewera omwe anagenda pa mchitidwewu.
Iwo atinso adabwa ndi kuthamangitsa milandu pa nkhani ya FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers pomwe mwa zina, Bullets inakonza bus ya Silver komabe ayilipilitsa ndalama yoonjezera pomwe Dedza
"TIKUYENERA KUTI TIONE CHITSOGOLO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yawo ikungoyenera kuvomereza kuti agonja ndipo ayang'ane chitsogolo kuti akonze mavuto omwe akumana nawo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya FOMO FC pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati mpira unawavuta zomwe zachititsa kuti agonje mmasewerowa.
"Tagonja tivomereze zinthu zinativuta mmasewerowa nde tikungoyenera kuti tibwerere tikakonze mavuto athu kuti chitsogolo tiyende bwino nde tivomereze zativuta lero." Anafotokoza Mwansa.
Iye anati akudziwa kuti akhumudwitsa otsatira awo koma akungoyenera kuti adekhe bwinobwino poti iwo akuyang'ana chitsogolo kuti zinthu ziziyenda bwino ndipo azipambana mmasewero awo.
Timu ya Moyale ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe tsopano ili ndi mapointsi 14 pa masewero khumi ndi amodzi (11) omwe asewera.
MOYALE YAPEZA BWENZI LOSAONA NYENGO
Kampani ya Medical Aid Society of Malawi (MASM) yapereka thandizo la unifolomu kutimu ya Moyale Barracks yomwe agwiritse mu ligi ya chaka chino.
Izi zadziwika kudzera pa tsamba la mchezo la Facebook la timuyi ndipo mwambowu unachitikira ku Mzuzu lachisanu.
Kampaniyi yapereka unifolomu yovala pakhomo, koyenda komanso ma track suit ku timuyi.
Timu ya Moyale Barracks ikuyembekezeka kuyima pachulu ndi kulengeza bwenzi lawo latsopano lomwe liziwathandiza mu ligi ya chaka chino ku mmawaku.
Timuyi yatsimikiza kudzera pa tsamba la mchezo la Facebook kuti litchule kampaniyi mmaola akudzawa.