Bullets ikuyamba ndi Creck mu Sapitwa
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets iyamba masewero awo ndi Creck Sporting Club mu mpikisano wa Sapitwa Big Four wa chaka cha chino.
Izi zadziwika pa Mayere omwe a achitika lachiwiri ku mmawa ndipo matimu onse anayi adziwa momwe ayambire.
Timu ya Mighty Tigers yomw ndi yokha imene inalikonso chaka chatha ikuyamba mpikisanowu ndi timu ya Ekhaya yomwe yalowa kumene mu Supa ligi nthawi ya 12:00hrs.
Ndipo 3 koloko, Bullets idzalowa m'bwalo ndi timu ya Creck ndipo opambana pa masewero awiriwa adzafika mu ndime yotsiriza.
Masewerowa ayamba loweruka pa 23 March ndipo ndime yotsiriza iliko pa 24 March lomwe ndi lamulungu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores