Wosewera wotchinga pagolo wa Nyasa Big Bullets, Richard Chimbamba wayamikila ubale wabwino womwe ulipo pakati pa iye ndi timuyi kuyambira kumabwana komanso m'phunzitsi wa timuyi.
Chimbamba walankhula izi pamene Bullets yawonjezera gwilizana wake ndi iye kwazaka zina ziwiri.
Iye wati izi zimpatsa mangolomera atsopano ndipo watsimikiza kuti apitiliza kudzipeleka potumikila timu yake.
Powonjezera apa, Chimbamba wachenjeza onsewera anzake omwe akubwera kumene kutimuyi kuti ayenera kukhala amwambo kaamba kakuti izi ndizomwe zimathandizila kukhalitsa pa malo monga momwe zakhalira kwa iye ndi Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores