"LERO ANTHU AKHUMUDWA TITASWA BULLETS" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Elvis Kafoteka, wati timu yake ili ndi osewera abwino kwambiri zomwe zikuwapatsa mtima oti masewero omwe atsala nawo pakhomo onse adzachita bwino ndipo ayambira ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe ali pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati timu yake ikuyenera kuyikapo mtima osati ingodalira kuti ili pakhomo komabe mtima omwe uli mwa osewera ake Bullets ilira ndithu.
"Anthu ena amati tituluka koma FOMO inalira pomwepa komanso matimu ena akuluakulu anafapo nde sindikukhulupilira kuti timu ina ibwera kudzatimenya pano ayi ndipo tiyambira kumenya Bullets." Anatero Kafoteka.
Iye watinso timuyi itsalirabe mu ligiyi pomwe wati FOMO ndi dzina lalikulu lomwe iye ngati mphunzitsi komanso osewerawa akuyenera kuyifera ndithu.
Iwo ali pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) ndi mapointsi okwana 25 pa masewero 27 omwe yasewera ndipo ikutsala ndi mapointsi awiri kuti idutse Bangwe Al
Mutumizile pa 0981511741
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores