"KB YABWERETSA MPHUNZITSI WABWINO" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati masewero atimu yake ndi Kamuzu Barracks akhala ovuta kwambiri poti anzawowa abweretsa mphunzitsi woonjezera Temwa Msukwa yemwe iyenso amamupatsa ulemu kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo la Silver ndipo wati timu yake ikufunitsitsa kuti ipate mapointsi atatu kuti ipitilire kupita patsogolo mu ligi.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti KB ndi timu yabwino kwambiri ngakhale mchigawo choyamba inatidzidzimutsa ndi zigoli ziwiri koma tinayesetsa tinabwenza nde akhala ovuta koma ifeyo takonzeka kwambiri." Anatero Mponda.
Iye anati Msukwa ndi mmodzi mwa aphunzitsi omwe amalimbikitsa osewera ake kuti azimenyabe nkhondo komabe iwo akonza mavuto omwe akumana nawo mmasewero omwe amasewera kuti achite bwino pa masewerowa.
Silver ili pa nambala yoyamba mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 45 pa masewero 19 omwe iwo asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores